‘Oonekera Monga Mauniko’
1 M’kati mwa mdima wauzimu ndi wamakhalidwe wa dongosolo la zinthu lino, olambira Mulungu woona, Yehova, oposa sikisi miliyoni ‘akuonekera monga mauniko’ m’mayiko okwana 234 padziko lonse lapansi. (Afil. 2:15) Zimenezi zimachititsa kuti tizioneka mosavuta. Kodi timasonyeza bwanji kuunika kwa choonadi kwa mtengo wapatali kochokera kwa Yehova?—2 Akor. 3:18.
2 Zochita Zathu: Anthu amaona msanga khalidwe lathu. (1 Pet. 2:12) Mkazi wina anati wa Mboni yemwe anali kugwira naye ntchito anali wokoma mtima ndiponso wothandiza ndipo sanali kutukwana kapena kuseka nthabwala zosayenera. Pamene ena anali kufuna kum’puta wa Mboniyo mwakugwiritsa ntchito mawu olaula iye ali pomwepo, sananene chilichonse koma molimba mtima anachitabe zinthu zabwino. Kodi zimenezi zinam’khudza motani mkaziyo? Iye anati: “Khalidwe lake linandisangalatsa kwambiri moti ndinayamba kufunsa mafunso okhudza Baibulo. Ndinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu ndipo m’kupita kwanthaŵi ndinabatizidwa.” Mkaziyo anawonjezera kuti: “Khalidwe lake ndi limene linandichititsa kupenda zomwe Mboni za Yehova zimakhulupirira.”
3 Mmene timachitira ndi olamulira, mmene timaonera zochitika zadziko ndiponso zolankhula zathu zabwino zimatichititsa ife Mboni za Yehova kuoneka monga anthu amene amatsatira miyezo yapamwamba ya Baibulo. Ntchito zabwino zimenezi zingabweretse ulemerero kwa Yehova ndiponso kukopa anthu ena kuti am’lambire.
4 Mawu Athu: N’zoona kuti anthu amene amaona khalidwe lathu labwino sangadziŵe chifukwa chake ndife osiyana ngati sitiwauza zimene timakhulupirira. Kodi amene mumagwira nawo ntchito kapena anzanu a kusukulu amadziŵa kuti ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova? Pokambirana nkhani zina, kodi mumayesa kugwiritsa ntchito mpatawo kuwalalikira? Kodi n’cholinga chanu ‘kuŵalitsa kuunika kwanu pamaso pa anthu’ panthaŵi iliyonse yoyenera?—Mat. 5:14-16.
5 Kukwaniritsa ntchito yathu monga mauniko kumafuna mtima wodzipereka. Kufunitsitsa ndi mtima wonse kudzatichititsa kusiya zinthu zosafunika kuti tichite zambiri m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira.—2 Akor. 12:15.
6 Mwa zochita zathu ndiponso mawu athu, tiyeni tipitirize kuonekera monga mauniko. Tikatero, anthu ena angalimbikitsidwe kulemekeza Yehova limodzi nafe.