Mbiri Yateokrase
◼ Maiko a ku West Africa a Benin, Cameroon, Côte d’Ivoire, Ghana, Liberia, ndi Nigeria onsewo m’February anafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa.
◼ Anthu ambiri amene anathaŵa nkhondo ku Liberia tsopano akubwerera kwawo, ndipo m’dziko limenelo mulidi njala ya choonadi. Chiŵerengero chawo chapamwamba cha ofalitsa 2,286 m’February anapereka lipoti la maphunziro a Baibulo a panyumba okwana 6,277.
◼ Ofalitsa a ku Macao anawonjezeka ndi 16 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha, okwanira 135 anapereka lipoti m’February.
◼ Ku South Pacific, Fiji, Solomon Islands, ndi Tahiti, onsewo m’February anapereka lipoti lachiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa.
◼ Chilumba cha Madagascar chinafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 9,484, kumeneku kunali kuwonjezeka ndi 14 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha. Ndipo m’February anaperekanso lipoti la maphunziro a Baibulo a panyumba oposa 20,000.