Mbiri Yateokalase
Zilumba za Marshall: M’February chiŵerengero chonse cha ofalitsa chinali 203—chiwonjezeko cha 4 peresenti kuposa chiŵerengero cha chaka chatha mwezi womwewo!
Norway: M’February 1999, apainiya othandiza anawonjezeka mpaka 72 peresenti kuposa a m’February 1998; apainiya okhazikika, 9 peresenti; maulendo obwereza, 4 peresenti; ndipo maphunziro a Baibulo, 6 peresenti. Mabuku ndi mabolosha ogaŵiridwa anawonjezerekanso.
Romania: Panali chiwonjezeko chachikulu m’ntchito ya apainiya ndi m’chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo amene anali kuchititsidwa, komanso m’February anali ndi chiŵerengero chatsopano chapamwamba cha ofalitsa 37,502.