Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/98 tsamba 8
  • Ndikufuna Phunziro la Baibulo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndikufuna Phunziro la Baibulo!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kuyambitsa Maphunziro m’Bolosha la Mulungu Amafunanji
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Ndilo Tiziphunzitsira Anthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 11/98 tsamba 8

Ndikufuna Phunziro la Baibulo!

1 Ambiri a ife tasonyezapo chikhumbo chofuna phunziro la Baibulo, ndipo pali chifukwa chabwino. Timakwaniritsa cholinga chathu cha kupanga ophunzira atsopano mwa ntchito imeneyi ya maphunziro a Baibulo. (Mat. 28:19, 20) Komatu ambiri a ife tatha miyezi ingapo, mwinanso zaka, tisanapeze chimwemwe chapadera chimene chimadza pophunzitsa munthu wina choonadi. Kodi tingachitenji pa zimenezi mu November muno? Popeza kuti mwezi uno tikugaŵira buku la Chidziŵitso, tingayesetse mwapadera kuti tiyambitse maphunziro a Baibulo atsopano ndi bukuli.

2 Patulani Mapeto a Mlungu Umodzi kapena Yoposerapo: Tikulimbikitsa aliyense kuti apatule nthaŵi mwezi uno yoti asumike maganizo pa kuyambitsa phunziro la Baibulo latsopano. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ayenera kusankha mapeto a mlungu kapena milungu yoti igwiritsidwe ntchito kokha pa chifuno chimenechi ndiyeno nkulinganiza magulu awo kuti ayesetsedi kugwira ntchito yopanga maulendo obwereza.

3 Popita kumisonkhano imeneyi yokonzekera utumiki, tengani zolembapo zanu za maulendo obwereza. Ndiyeno bwererani kwa onse aja amene anasonyeza chidwi, anatenga mabuku, kapena anafika pamisonkhano. Fikirani aliyense ndi cholinga chenicheni cha kuyambitsa phunziro.

4 Chitani Chitsanzo cha Phunziro la Baibulo: Pamisonkhano yosankhika yokonzekera utumiki, muyenera kuchita chitsanzo chokonzedwa bwino, kusonyeza mmene mungayambire phunziro pa ulendo wobwereza. Munganene kuti: “Anthu ambiri ali ndi Baibulo koma sadziŵa kuti lili ndi mayankho a mafunso ofunika amene tonsefe timakhala nawo pamoyo wathu. [Msonyezeni mpambo wa zamkati mwa buku la Chidziŵitso, ndi kuŵerenga mitu ya machaputala 3, 5, 6, 8, ndi 9.] Mwa kugwiritsa ntchito chothandizira kuphunzira chimenechi kwa ola limodzi kapena kuposerapo pamlungu, mungalizindikire Baibulo m’miyezi yoŵerengeka chabe. Ngati mungasankhe mutu umodzi mwa imeneyi, mokondwera ndingakusonyezeni mmene pologalamu yake imakhalira.” Ngati munthuyo akunyinyirika kuti aphunzire chifukwa cha kukhala wotanganidwa, mfotokozereni kuti tilinso ndi pologalamu yachidule. Msonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji ndi kumpempha kuphunzira phunziro limodzi lachidule pamlungu kwa mphindi 15-30.

5 Ngati tonse mogwirizana tiyesetsa kuyambitsa maphunziro ndipo ngati tipempherera madalitso a Yehova pa zoyesayesa zathu, ndithudi tipeza maphunziro atsopano! (1 Yoh. 5:14, 15) Ngati mukufuna phunziro la Baibulo, uwu ungakhale mwayi wanu woti muliyambitse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena