Kuwonjezera Umboni Pamene Mapeto Akuyandikira
1 Nyengo yotuta ndi nthaŵi yosangalatsa kwambiri. Komanso ndi nthaŵi ya ntchito yambiri. Pali nthaŵi yake yosonkhanitsa mbewu. Antchito sayenera kuchita ulesi pantchito yawo.
2 Mophiphiritsa, Yesu anayerekezera “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano” ndi nthaŵi yotuta. (Mat. 13:39) Tikukhala m’nthaŵi yamapeto a dongosolo la zinthu lilipoli, ndipo kwatsala nthaŵi yochepa yopereka umboni “padziko lonse lapansi.” (Mat. 24:14) Pamene mapeto akuyandikira pafupi kwambiri, tiyenera kuwonjezera mbali yathu mu utumiki. Chifukwa chiyani? Yesu anati: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.”—Mat. 9:37, 38; Aroma 12:11.
3 Ichiteni Mwachangu: Pamene Yesu anayamba ntchito yake yaikulu yolalikira, anali ndi zaka zitatu ndi theka zokha kuti achite zimene anatumidwa. Analalikira mwachangu, akumati: ‘Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu chifukwa ndinatumidwa kudzatero.’—Luka 4:43.
4 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake changu chofananacho. (Marko 13:32-37) N’chifukwa chake ‘masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira za Kristu Yesu.’ (Mac. 5:42) Zinthu zosafunika kwenikweni sizinakhale zoyamba m’miyoyo yawo. Ngakhale kuti anali oŵerengeka, anali okhoza kulalikira uthenga wabwino kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:23.
5 Palinso chifukwa chachikulu chotipangitsa ife kukhala ndi changu chofananacho tsopano, popeza “chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” (1 Pet. 4:7) Yehova waika tsiku ndi ola lochotsa dongosolo la zinthu lilipoli. (Mat. 24:36) Ntchito yolalikira imalizidwa m’nthaŵi imene yatsalayi. N’chifukwa chake tiyenera kupitiriza kuwonjezera zoyesayesa zathu kuti tifikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino.
6 Mwa kuwonjezera mbali yathu m’ntchito yochitira umboni pamene mapeto akuyandikira, tidzakhala osangalala kunena kwa Yehova, monga momwe ananenera Yesu kuti: ‘Tatsiriza ntchito imene munatipatsa kuchita.’—Yoh. 17:4.