“Lalikira Mawu . . . Mwachangu”
1 Ngati mulandira chinthu cholembedwa kuti “MUCHITE CHANGU,” kodi mumachiona motani? Mawu akuti “changu” amatanthauza “chofunika kuchichita nthaŵi yomweyo.” N’chifukwa chake, mtumwi Paulo analangiza Akristu ‘kulalikira mawu . . . [mwachangu, NW].’ (2 Tim. 4:2) Kodi mumalabadira mwa kuichita ntchito imeneyi nthaŵi yomweyo?
2 Mwinamwake Paulo anauzidwa kuti abale ake ena anali n’chizoloŵezi chosonyeza ‘ulesi m’machitidwe awo’ monga Akristu. (Aroma 12:11) Izi zinalepheretsa ntchito yawo kukhala ndi zotsatira zake komanso chimwemwe chimene akanapeza mwa kuthandiza ena.
3 Mmene Yesu Amaonera Utumiki: Yesu anakondadi kuchita utumiki wake! Anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” Chitsanzo cha Yesu chinasonkhezera ophunzira ake, amene anawalimbikitsa mwa kuwauza kuti ‘m’minda mwayera kufikira kumweta.’ (Yoh. 4:34, 35) Changu chimene anasonyeza mu utumiki wake wonse chinaoneka pamene anauza ophunzira ake ‘kupempha Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.’ (Mat. 9:38) Yesu anadziŵa kuti ntchito yake inali yolalikira, ndipo anatsimikiza mtima kusalola china chilichonse kumulepheretsa kuigwira.
4 Bwanji Ife? Kuposa kale lonse, lerolino pakufunika kuchita changu zedi kuti tipite patsogolo ndi ntchito yolalikira. M’madera ambiri a dziko, minda yayera kufikira kumweta. Ngakhale m’mayiko ooneka kuti alalikiramo mokwanira, chaka chilichonse mumapezeka anthu zikwizikwi akubatizidwa. Popeza mapeto a dongosolo la zinthu lino akuyandikira mofulumira, pali zochita ‘zochuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Kuposa kale lonse, n’kofunika kuti tichite khama ndithu kuuza ena uthenga wa Ufumu.
5 Tiyeni titangwanike kwambiri kuuza ena uthenga wabwino, kunyumba ndi nyumba ndiponso kwina kulikonse kumene kungapezeke anthu m’gawolo. Mwa kugwira nawo ntchito yolalikira mokwanira, timasonyeza bwino lomwe kuti taika Ufumu patsogolo m’moyo wathu. (Mat. 6:33) Kukhulupirika kwathu polalikira mawu mwachangu kudzatipatsa chimwemwe chachikulu.