Konzekereranitu!
1 Gulu la Yehova limapereka pologalamu yanthaŵi zonse ya zochitika zateokalase zokonzedwa kuti zikwaniritse zosoŵa zathu zauzimu. Kuyamikira kumatisonkhezera kugwiritsa ntchito mokwanira zonse zimene zimakonzedwa, monga kuchezeredwa ndi woyang’anira woyendayenda, misonkhano yadera ndi misonkhano yachigawo, komanso zochitika zina zapadera zomwe zimakonzedwa pampingo. (Mat. 5:3) Komabe, ena amalephera kupindula ndi makonzedwe auzimu ameneŵa chifukwa cha zinthu zimene akonza kuti achite. Kodi tingachite chiyani kuti tipeŵe zimenezi? Tingatsimikize motani kuti zinthu zimene sizili zateokalase sizikudodometsa “zinthu zofunika kwambiri.”—Afil. 1:10, NW.
2 Kuganiza Mwanzeru n’Kofunika: Miyambo 21:5 imatilimbikitsa kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphaŵi.” Kuti ‘tichulukitsedi katundu’ wauzimu, tiyenera kukonzekereratu mwakhama, tikumakumbukira zochitika zateokalase zomwe zakonzedwa. Kuti tipeze madalitso auzimu tiyenera kuika zochita zaumwini panthaŵi yomwe sizitilepheretsa kukapezekapo. Ngati tikonza mothamanga zinthu zaumwini zomwe tikufuna kuchita, popanda kuganizira zochitika zateokalase zomwe zakonzedwa, n’kodziŵikiratu kuti tidzakhala ‘amphaŵi’ mwauzimu.
3 Osaphonya! Tonse timakonzekera za m’tsogolo, kuphatikizapo masiku atchuthi, maulendo antchito, kukayendera achibale, ndi zina zotero. Musanakonze kapena musanatsimikize zomwe mukufuna kuchita, onani ndandanda ya zochitika zauzimu zomwe zili m’tsogolo. Ngati mupeza kuti woyang’anira dera akubwera kapena kuti nthaŵi imene inu simudzakhalapo kudzakhala msonkhano wadera, yesetsani kukonzanso zochita zanu kotero kuti mudzathe kupezekako. Amatiuziratu zochitika zikuluzikulu zomwe zichitike patsogolopa. Akulu a mpingo wanu angakuuzeni zimene zakonzedwa mumpingo wanu.
4 Mwa kuchita mwanzeru ndi kukonzekereratu zinthu zofunika kwambiri, ‘tidzadzala nacho chipatso cha chilungamo, . . . kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.’— Afil. 1: 11.