Mbiri Yateokalase
◼ Armenia: Lipoti la December linali ndi ofalitsa 4,741 aliyense anali ndi avareji ya maola 16 mu utumiki. Chiŵerengero chapamwamba chatsopano chimenechi cha ofalitsa chawonjezeka ndi 17 peresenti pa avareji ya chaka chatha.
◼ Chile: Ofalitsa anasangalala pamene anamva za maola atsopano ofunika kwa apainiya, zimenezi zaoneka m’chiŵerengero chapamwamba choposa ziŵerengero zina zonse cha apainiya okhazikika 4,351 amene anapereka lipoti mu January. Komanso, ofalitsa 5,175 anapereka lipoti monga apainiya othandiza, chiŵerengero chabwino kwambiri m’chaka chino chautumiki.
◼ Ukraine: Mwa ofalitsa 100,129 amene anapereka lipoti mu January, 12 peresenti anali mu utumiki wa nthaŵi zonse. Ukraine inali ndi apainiya okhazikika 5,516—chiŵerengero chapamwamba cha nambala 27—ndipo ofalitsa ena 6,468 anapereka lipoti monga apainiya othandiza.