Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/99 tsamba 1
  • Maphunziro Akusukulu ndi Zolinga Zanu Zauzimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maphunziro Akusukulu ndi Zolinga Zanu Zauzimu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro Okhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
    Galamukani!—1998
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 8/99 tsamba 1

Maphunziro Akusukulu ndi Zolinga Zanu Zauzimu

1 Kupeza maphunziro oyambirira abwino udakali wamng’ono kungakupatseni maluso apamwamba ofunika kwa inu kuti mudziŵe kuŵerenga ndi kulemba bwino ndiponso kuti mudziŵe za dziko, mbiri, masamu, ndi sayansi. Mwa kutero, mungaphunzire kuganiza bwino, kupenda mfundo, kuthetsa mavuto, ndi kupeza malingaliro othandiza. Maphunziro amenewo adzakuthandizani kwambiri m’moyo wanu wonse. Kodi maphunziro anu akusukulu ndi zolinga zanu zauzimu m’moyo zikugwirizana motani ndipo zingakuthandizeni bwanji kupeza “nzeru yeniyeni ndi kulingalira”?—Miy. 3:21, 22.

2 Khalani Wothandiza mu Utumiki wa Mulungu: Mudakali kusukulu, tcherani khutu m’kalasi ndipo chitani bwino lomwe homuweki yomwe mwapatsidwa. Ngati muzoloŵera kuŵerenga bwino ndi kuphunzira, mungasanthule mosavuta Mawu a Mulungu ndi kukhala wolimba mwauzimu. (Mac. 17:11) Chidziŵitso chokwanira chidzakuthandizani kulankhula ndi anthu osiyana mikhalidwe, zokonda, ndi zikhulupiriro pamene mwakumana nawo mu utumiki. Maphunziro amene mumapeza kusukulu adzakhala othandiza pamene mukusamalira maudindo anu achikristu m’gulu la Mulungu.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:21; 4:11.

3 Phunzirani Kudzithandiza Nokha: Ngati mudzipereka, mungaphunzirenso maluso ofunika kupeza zofunika m’moyo mukatha maphunziro anu akusukulu. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:8.) Sankhani maphunziro oti muphunzire mosamala. M’malo molimbikira maphunziro amene ntchito yake ili yosoŵa, lingalirani zophunzira ntchito ya manja kapena luso limene lidzakuthandizani kupeza ntchito yabwino kulikonse. (Miy. 22:29) Maphunziro amenewo adzakutheketsani kuti muthe kudzithandiza nokha ngati mungafune zokatumikira kumalo amene ali ndi kusoŵa kokulira.—Yerekezerani ndi Machitidwe 18:1-4.

4 Kupeza maphunziro abwino oyambirira akusukulu kungakuthandizeni kuwonjezera utumiki wanu. Limbikirani kuti mupeze maluso ofunika kuti mudzazithandize nokha pamene mukupita patsogolo mu utumiki wa Yehova. Choncho kuphunzira kwanu kudzakhala ngati chida chokuthandizirani kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena