Kodi Mukuyamikira Chikondi cha Kristu?
1 Pokumbukira njira ya moyo ya Mbuye wake, mtumwi Yohane analemba kuti: “[Yesu] mmene anakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yoh. 13:1) Panyengo ya Chikumbutso ino, malingaliro athu amakhala pa chikondi chimene Kristu anasonyeza. Tingayamikire chikondi chimenecho mwa kusonyeza chikhulupiriro mu dipo, kuchita ntchito yolalikira mwachangu, ndiponso kupirira “kufikira mapeto” monga anachitira Yesu.—Mat. 24:13; 28:19, 20; Yoh. 3:16.
2 Kuyamikira Chikondi cha Kristu: M’mlungu womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi, Yesu anali wachangu kwambiri. (Mat. 21:23; 23:1; 24:3) Monga otsanzira Kristu, ifenso timasonkhezeredwa ndi chikondi kuti ‘tiyesetse’ mwamphamvu muutumiki wa Yehova. (Luka 13:24) Kodi mungapezerepo mwayi pamakonzedwe a ntchito yochitira umboni yowonjezereka m’mwezi wa April mwakuwonjezera nthaŵi imene mumakhala mu utumiki?
3 Chaka chino Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chidzakhalapo Lachitatu madzulo, pa April 19. Kodi ndi angati amene adzapezeke pamwambo wapadera umenewu? Mbali yaikulu, zimenezo zidzadalira ife. Kodi mwalemba ndandanda ya amene mukufuna kuwaitana—ophunzira Baibulo anu ndi anthu ena okondwerera, achibale, ogwira nawo ntchito, ndi anzanu akusukulu? Kodi mwawafikira ndi kuwauza kuti ali olandiridwa ndi manja aŵiri? Kodi mudzawakumbutsa patatsala masiku angapo kuti chikumbutso chichitike? Kodi akufunika kuti muwathandize kukafika kumaloko? Akulu akuitananso aliyense amene wakhala wofooka mu utumiki. Popeza kuti Chikumbutso chidzachitika madzulo patsiku lam’kati mwa mlungu osati kumapeto a mlungu, izi sizikutanthauza kuti sikofunika kuti onse adzapezekepo.
4 Bwerani Okonzeka: N’kofunika kukhala okonzeka ndiponso kukhala ndi malingaliro oyenera pamene tili pa Chikumbutso. Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kukumbukira kufunika kwa mwambo umenewu. (1 Akor. 11:20-26) Mungaŵerenge uthenga wabwino wa Yohane machaputala 13 mpaka 17 panthaŵi ya phunziro lanu la Baibulo labanja ndiyeno n’kuuza aliyense m’banjamo kulankhulapo zimene nsembe ya Yesu imatanthauza kwa iye. Osaiwala kuŵerenganso Baibulo kwa mlungu wa Chikumbutso tsiku ndi tsiku!
5 Kukonda kwathu Kristu n’kozama ndipo kudzapitirira pa April 19. Tatsimikiza mtima kuti tidzasonyeza kum’konda nthaŵi zonse! Chikumbutso cha chaka chino chidzatithandiza kulimbitsa chosankha chimenechi.