Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/00 tsamba 3
  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu” wa 1994
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa “Atamandi Achimwemwe”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 7/00 tsamba 3

Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?

1 Titafunsidwa ngati timayamikira zinthu zopatulika, mosakayikira tidzayankha mofulumira kuti eee! Kodi zina mwa zinthu zopatulika za Mulungu zimene timayamikira n’ziti?

2 Si mmene timayamikirira unansi umene tili nawo ndi Atate wathu wakumwamba! Amatitsimikizira kuti ngati ‘tiyandikira kwa iye, iye adzayandikira kwa ife.’ (Yak. 4:8) Pakanapanda nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, palibe akanalandira moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Kuti tisonyeze kuyamikira kochokera pansi pa mtima, tsiku lililonse timatchula m’pemphero kuyamikira kwathu konse mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu imeneyi.

3 Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo Lopatulika, n’lopatulikanso kwa ife, monga mmene lilili gulu la Yehova lapadziko lapansi. Mwakukhala mogwirizana ndi mfundo za Baibulo zachikhalidwe, kulimbitsa chikondi cha pa abale, kutsatira malangizo a teokalase, ndiponso kumvera anthu otitsogolera timasonyeza kuyamikira kwenikweni dongosolo lochokera kwa Yehova limeneli.—1 Pet. 1:22.

4 Timalandira chakudya chochuluka chauzimu kudzera mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Tikaona tokha zimenezi chaka chino pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu.” Kumeneko tikalandira malangizo ofunikira ndiponso kusangalala ndi mayanjano okoma amene timawafuna kwambiri. Ndi motani mmene tingasonyezere kuyamikira kwathu konse dongosolo lopatulika limeneli?

5 Musanyalanyaze Nyumba ya Yehova: Nehemiya anapempha awo amene anagwira ntchito molimbika kumanganso malinga a Yerusalemu kuti ‘asasiye nyumba ya Mulungu wawo.’ (Neh. 10:39) “Nyumba” ya Yehova ndiyo dongosolo lake la kulambira. Misonkhano yathu yachigawo ndi mbali ya dongosolo limeneli. Kuti tisanyalanyaze dongosolo limeneli, tiyenera kukapezekapo ndi kutchera khutu kwambiri, kum’sonyeza Yehova kuti timayamikira kwambiri zogaŵira zake. (Aheb. 10: 24, 25) Kodi pakalipano tiyenera kukonzekera chiyani kuti tisonyeze kuti timayamikira kwambiri chochitika chopatulika chimenechi?

6 Kapezekenipo Masiku Onse Atatu: Aliyense wa ife ayenera kukonza kukapezekapo masiku onse atatu a msonkhano. Kodi mukukonzekera kumakafika mofulumira tsiku lililonse ndi kukhalapo mpaka Lamlungu papemphero lomaliza? Ngati ndi choncho, mudzapeza madalitso ochuluka. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kupezeka pamsonkhano. Kutsanzika kuntchito yolembedwa kungafune kukhala wolimba mtima. Nthaŵi zina zoyendera zingakhale zovutirapo. Koma musalole zinthu zimenezi kukulepheretsani kupezeka pamsonkhano.

7 Onani Chitsanzo Chabwino Kwambiri Ichi: M’dziko lina mu Africa kumene kuli nkhondo yapachiweniweni, gulu la abale lili paulendo wopita kumsonkhano wachigawo wachaka chatha, linakumana ndi gulu la asilikali. Abalewo anafunsidwa kuti: “Ndinu ndani, ndipo mukupita kuti?” “Ndife Mboni za Yehova, ndipo tikupita ku msonkhano wachigawo,” anayankha motero. Mmodzi mwa asilikaliwo anati: “Inu a Mboni za Yehova simuopa kanthu. Kazipitani, ndipo mukachita msonkhano wanu popanda chovuta chilichonse. Komabe, dziŵani kuti mukumana ndi asilikali ambiri. Muzingoyenda pakatikati pa msewu! Mukaona anthu ambiri atasonkhana, inu muzingoyendabe pakatikati pa msewu!” Abalewo anachita zimenezi ndipo anakafika bwinobwino kumsonkhano. Abale ameneŵa anapindula chifukwa chakuti anasonyeza kuyamikira zinthu zopatulika.

8 Monga abale athu amenewo, ifenso timakumana ndi mavuto. Koma mosakayikira, tingatsanzire chikhulupiriro chawo ndipo tingatsimikize kukapezekapo pazigawo zonse za msonkhano wathu wachigawo. Ngati pakufunika kusintha zinthu zina, pemphani Yehova kuti akutsogozeni, podziŵa kuti adzadalitsa khama lathu kuti tikapezeke papulogalamu yonse.

9 Pezani Madalitso: Timalakalaka Mawu a Mulungu, popeza kupyolera mwa iwo tikapeza chipulumutso. (1 Pet. 2:2) Kupezeka kwathu pa msonkhano wachigawo ndiponso kumvetsera ku nkhani kudzathandiza aliyense wa ife kukhala ndi chikhulupiriro cholimba m’Mawu ameneŵa ndipo titha kupirira bwinobwino ziukiro za Satana. Mwakutero, tidzam’sonyeza Yehova ndi anthu onse otiona kuti timayamikira kwambiri zinthu zopatulika ndi kuti “si ndife a iwo akubwerera . . . koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”—Aheb. 10:39; 12:16; Miy. 27:11.

10 Tingayembekezere Yehova Mulungu kutsegula mazenera akumwamba ndi kutitsanulira madalitso auzimu ochuluka kwambiri. (Mal. 3:10) Chikhaletu cholinga chanu kukapezeka pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu” kuyambira tsiku lotsegulira msonkhanowu Lachisanu m’maŵa mpaka madzulo a Lamlungu papemphero lomaliza n’kunena nawo kuti “Amen!” Mudzasangalala kuti sizinakupiteni!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena