Bokosi la Mafunso
◼ Kodi akalinde angawathandize motani makolo kuthandiza ana awo kukhala a khalidwe labwino pamisonkhano?
Mwachibadwa ana amakhala ojijirika, osazoloŵera kukhala pansi kwanthaŵi yaitali. Misonkhano ikatha, ana amakhala ochangamuka kwambiri ndipo kumawapangitsa kuthamangathamanga ndi kuthamangitsana mu Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse osonkhanira. Komabe, mwambi uwu n’ngoona, “mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.”—Miy. 29:15.
N’zachisoni kuti, abale ndi alongo athu ena achikulire avulala kwambiri chifukwa chakuti ana anawakola n’kugwa. Izi zachititsa mavuto osafunikira komanso zawonongetsa mosayenera ndalama za makolo ndiponso za mpingo. Kuti iwo atetezeke ndiponso anthu ena, ana sayenera kuloledwa kuthamanga ndi kuseŵera m’kati kapena kunja kwa Nyumba ya Ufumu.
Makolo ali ndi udindo wa m’Malemba wophunzitsa ana awo kulemekeza malo olambirira. (Mlal. 5:1a) Pamisonkhano yathu yachikristu, misonkhano yadera, ndiponso yachigawo, akalinde ali ndi udindo woona kuti ‘zonse zikuchitika moyenera ndi molongosoka’ ndikuti pali “makonzedwe.” (1 Akor. 14:40; Akol. 2:5) Ayenera kukhala atcheru mapulogalamu asanayambe, ali m’kati ndiponso akatha, mu holo ndi kunja kwa holo komwe. Ngati mwana akuthamangathamanga kapena akuchita mphulupulu, kalinde angaimitse mwanayo mwachikondi, n’kumufotokozera chifukwa chake makhalidwe oterowo sali oyenera. Makolo a mwanayo ayeneranso kuuzidwa mwachikondi za vuto la mwanayo ndi kufunika koyang’anira mwanayo. Makolo ayenera kuchitapo kanthu pa zimenezi.
N’zoona kuti nthaŵi zina makanda ndiponso ana ang’onoan’gono akhoza kulira kapena kuvutitsa misonkhano ili m’kati. Akalinde, ofika mofulumira ku holo kutatsala mphindi 20 kuti mapulogalamu ayambe, angasunge mizere iŵiri ya kumapeto kaamba ka makolo amene angafune kukhala kumeneko ndi ana awo ang’onoang’ono. Ena tonse timvere zimenezi mwa kuwasiyira anthu ameneŵa malowo.
Ngati mwana akuvutitsa, makolo ayenera kuchitapo kanthu kenakake. Ngati makolo sakuchita kalikonse ndipo kuvutitsako kukudodometsa ena, kalinde ayenera kupempha khololo kupita naye panja mwanayo. Tikaitanira anthu atsopano amene ali ndi ana ang’onoang’ono ku misonkhano, tiyenera kukhala nawo pamodzi n’kumawathandiza kusamalira ana awo akamalira kapena kuvutitsa mwa njira ina iliyonse.
Zimatisangalatsa kuona ana azaka zosiyanasiyana pa Nyumba ya Ufumu ndi kuona khalidwe lawo labwino m’nyumba ya Mulungu. (1 Tim. 3:15) Mwa kulemekeza kwawo makonzedwe a Yehova akulambira, amam’lemekeza ndipo anthu onse mumpingo amawayamikira.