Bokosi la Mafunso
◼ Kodi n’chiyani chimene aliyense angachite kuti zizikhala zosavuta kuphunzira zinthu pamisonkhano ya mpingo? (Deut. 31:12)
Chifukwa cholemekeza Yehova ndiponso dongosolo limene wakhazikitsa kuti tizikhala ndi misonkhano, tonse timalimbikitsidwa kufika mwamsanga ndiponso kuti tizikhala okonzeka kuphunzitsidwa ndi iye. Ndi bwino kukhala m’mipando yakutsogolo kuti amene ali ndi ana ndiponso amene achedwa apeze malo mosavuta kumbuyo. Misonkhano isanayambe, zimitsani mafoni ndi zinthu zina zimene zingasokoneze anthu misonkhano ili mkati. Ngati aliyense atakhala ndi mtima wolemekeza misonkhano, sipangakhale zinthu zambiri zosokoneza ena.—Mlal. 5:1; Afil. 2:4.
Munthu wophunzira Baibulo akayamba kubwera kumisonkhano, ndi bwino kuti munthu amene akumudziwa mumpingomo azimutenga n’kukhala naye pamodzi. Zimenezi n’zofunika kwambiri ngati watsopanoyo ali ndi ana ofunika kuwaphunzitsa bwino kuti azimvetsera pamisonkhano. Mwina kungakhale kuyamba kuti banjalo lipezeke pamisonkhano. Motero makolo angakonde kukhala kumbuyo kuti asamasokoneze ena ngati atafuna kutuluka pang’ono ndi ana awo. (Miy. 22:6, 15) Mabanja amene ali ndi ana ang’onoang’ono asakhale panja popanda zifukwa zomveka, chifukwa akatero anawo amakhala omasuka kumachita phokoso. Nthawi zambiri zimakhala bwino kuti makolo angotuluka nawo anawo n’kukawalangiza kapena kuwasamalira kenako n’kubwerera.
Akalinde azionetsetsa kuti malo a misonkhano akulemekezedwa monga nyumba yolambiriramo. Iwo ayenera kuthandiza mabanja ndiponso anthu ena obwera mochedwa kupeza malo okhala. Akalindewo ayenera kusamala pothandiza anthu kupeza malo n’cholinga choti asasokoneze ena. Iwo ayenera kuchita zinthu mwanzeru pakachitika chilichonse mwadzidzidzi chosokoneza misonkhano. Ngati mwana wina akusokoneza pamisonkhano, akalinde ayenera kuthandizapo mwaulemu.
Onse opezeka pamisonkhano kudzalambira angathandize kuti zikhale zosavuta kuphunzira za Yehova ndi cholinga chake chobweretsa dziko latsopano lamtendere ndiponso lolungama.—Aheb. 10:24, 25.