Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/00 tsamba 4-5
  • Tcherani Khutu ku Mawu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tcherani Khutu ku Mawu a Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mvetserani ndi Kuphunzira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu” wa 1994
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 7/00 tsamba 4-5

Tcherani Khutu ku Mawu a Mulungu

1 Si zonse zimene anthu amalankhula zimafunika kuzimvetsera. Koma pamene Mulungu akulankhula, n’kofunika kwambiri kumvetsera. (Deut. 28:1, 2) Tikuyamikira kuti, olemba ouziridwa analemba “mawu a Mulungu” kaamba ka ubwino wathu. (Aroma 3:2) Msonkhano wachigawo ukubwerawu udzapereka mpata wapadera wakumva mawu a Mulungu ameneŵa akuŵerengedwa ndi kufotokozedwa. Ndi motani mmene mungakhalire wotchera khutu kwambiri?

2 Fikani Mofulumira M’maŵa Uliwonse: Tangolingalirani mmene Aisrayeli anasangalalira atauzidwa kukakumana ndi Yehova pa phiri la Sinai kuti akamve Chilamulo chake! (Eks. 19:10, 11, 16-19) Ngati mungakhale ndi malingaliro ofananawo pokalandira malangizo a Yehova pamsonkhano wachigawo, mudzakonza kufika mofulumira tsiku lililonse. Sitingamvetsere pulogalamu yonse ngati tifika mochedwa komanso n’kumasokoneza ena pamene tikuyang’ana malo okhala.

3 Ngakhale ena amene amafika mofulumira sakhala m’malo mwawo pulogalamu ikamayamba. N’chifukwa chiyani zimenezi zimachitika? Amadikira mpaka tcheyamani atchule nyimbo yotsegulira kuti aleke kukambirana ndi anzawo komanso kuti ayambe ulendo wopita m’malo mwawo. Tiyenera kudziŵa kuti mphindi zingapo nyimbo yotsegulira chigawo chilichonse isanayambe, tcheyamani adzakhala pansi ku pulatifomu nyimbo za Ufumu zoyamba zikuimbidwa. Ichi n’chidziŵitso choti ndi nthaŵi yoti tikhale pansi! Choncho, pamene akuti tiimbe nyimbo yotsegulira, tidzakhala okonzeka kuimbira nawo Yehova zitamando.

4 Mvetserani Monga Banja Limodzi: Aisrayeli ankati akasonkhana pamodzi kuwaŵerengera mawu a Mulungu, mabanja, ndiponso “ana aang’ono,” anayenera kumva ndi kuphunzira. (Deut. 31:12) Pamisonkhano yathu, ana safunika ‘kuwalekerera.’ (Miy. 29:15) Makolo, konzani kuti banja lanu lonse kuphatikizapo ana likhale pamodzi. Makolo ena amadikira mpaka nyimbo yotsegulira iyambe m’pamene amapita ndi ana awo kuchimbudzi. Komabe, izi sizingaphunzitse ana m’pang’ono pomwe kufunika kwa nyimbo ndi mapemphero pa kulambira kwathu. Ngati n’kotheka, n’kwabwino kwambiri kupita kuchimbudzi chigawo chilichonse chisanayambe!

5 Kugona mokwanira usiku uliwonse komanso kupeŵa kudya kwambiri nthaŵi yamasana kudzatithandiza kuti timvetsere. Ikani maganizo pa zimene wokamba nkhani akunena. Kanizani maganizo anu kuganiza zinthu zina. Ŵerengani nawo Baibulo pamene malemba akuŵerengedwa. Lembani mfundo zachidule. Nkhani iliyonse ikakambidwa, lingalirani m’mutu mwanu zimene wokamba nkhaniyo wanena, ndipo lingalirani mmene mungagwiritsirire ntchito mfundozo. Pamapeto a tsikulo, kambiranani pulogalamuyo monga banja. Ndi mfundo zotani zimene aliyense anasangalala nazo? Ndi motani mmene banja lanu lingagwiritsirire ntchito bwino chidziŵitso chimenechi?

6 Lemekezani Mawu a Mulungu: Misonkhano imatipatsa mipata yabwino yocheza ndi anzathu ndiponso kusangalala ndi mayanjano omangirira. Mwa kufika mofulumira, tidzakhala ndi nthaŵi yocheza mapulogalamu asanayambe. Komabe, ena amacheza mapulogalamu ali m’kati, akumaganiza kuti izi si zododometsa kwenikweni chifukwa tili m’holo yaikulu kwambiri. Ngakhale misonkhano ichitike m’malo aakulu, ndi nthaŵi yomvetsera, monga timachitira pamisonkhano ya m’Nyumba ya Ufumu. Kagwiritsidwe ntchito ka matelefoni a m’manja ndiponso makamera kasadodometse anthu mapulogalamu ali m’kati.

7 Pamene Mose ankalandira Chilamulo kuchokera kwa Yehova, “sanadya mkate kapena kumwa madzi.” (Eks. 34:28) Mofananamo, si koyenera kudya kapena kumwa mapulogalamu ali m’kati. Pokhapokha ngati pali vuto lalikulu la thanzi, ngati si choncho dikirani “nthaŵi yake” ya zimenezi.—Mlal. 3:1.

8 Malo ena amsonkhano, pakhalabe vuto la abale ndi alongo ambiri ngakhalenso ana akuyendayenda panja pa malo amsonkhano mapulogalamu ali m’kati. Akalinde adzalangizidwa kuuza anthu otereŵa kukakhala pansi m’malo awo. Antchito odzifunira a m’madipatimenti osiyanasiyana ayenera kukhala pansi mwamsanga akatha ntchito yawo. Ngati sanatumidwe kugwira ntchito mapulogalamu ali m’kati, ayenera kukhala pansi m’malo awo, ndi kumamvetsera mapulogalamu. Sayenera kukhala m’madipatimenti awo, n’kumayenderana mapulogalamu ali m’kati.

9 Sitikufuna kukhala ‘ogontha m’makutu’ pomvetsera Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:11) Chotero tiyeni titsimikize mtima kusonyeza ulemu woyenera mwa kumvetsera mwatcheru pamene mawu a Yehova akukambidwa pamsonkhano wathu wachigawo ukubwerawu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena