Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/13 tsamba 4
  • Mvetserani ndi Kuphunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mvetserani ndi Kuphunzira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Msonkhano Wachigawo wa mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 6/13 tsamba 4

Mvetserani ndi Kuphunzira

1. N’chifukwa chiyani tidzafunika kuyesetsa kuti timvetsere mwatcheru ndi kuphunzira pa msonkhano wachigawo?

1 Posachedwapa, misonkhano yachigawo ya chaka cha 2013 iyamba. Abale anagwira ntchito yaikulu pokonza pulogalamu yomwe ndi yothandiza kwambiri pa mavuto amene anthu padziko lonse akukumana nawo. Kodi inuyo mwakonzekera kudzapezekapo masiku onse atatu? Pa misonkhano ikuluikulu pamachitika zinthu zosiyanasiyana zomwe zingatidodometse. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti timvetsere pulogalamu yonse. Popeza chigawo chilichonse cha msonkhanowu chimakhala chachitali kuposa misonkhano ya mpingo, tiyenera kuyesetsa kuti maganizo athu asayambe kuyendayenda pulogalamu ili mkati. Komanso tikhoza kukhala otopa chifukwa cha ulendo wopita ku msonkhanoko ndiponso zinthu zina. Ndiye kodi tingatani kuti tidzakhalebe atcheru n’cholinga choti tidzamvetsere bwino ndi kuphunzira?—Deut. 31:12.

2. Kodi tingakonzekeretse bwanji mtima wathu kuti tidzapindule ndi msonkhano wachigawo?

2 Msonkhano Usanachitike: Pa webusaiti yathu ya www.pr418.com pali pulogalamu ya msonkhano wachigawo. Pa pulogalamuyi pamakhala mitu ya nkhani iliyonse yomwe idzakambidwe komanso lemba limodzi kapena awiri omwe ali ndi mfundo yaikulu ya nkhaniyo. Choncho ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti mungachite bwino kuoneratu zimenezi ndipo zikuthandizani kukonzekeretsa mtima wanu kuti mudzamvetsere bwino msonkhanowo. (Ezara 7:10) Pa Kulambira kwa Pabanja mungakambirane zokhudza msonkhanowu n’cholinga choti aliyense m’banja mwanu aziuyembekezera mwachidwi.

3. Kodi tingatani kuti tizidzamvetsera mwatcheru?

3 Msonkhano Uli Mkati: Ngati n’kotheka mungachite bwino kupitiratu ku chimbudzi msonkhano usanayambe. Komanso ngati muli ndi foni ya m’manja mungachite bwino kuizimitsa kuti isakusokonezeni ndiponso kuti musaigwiritse ntchito msonkhano uli mkati. Koma ngati pa zifukwa zina simukufuna kuzimitsa foni yanu, itchereni m’njira yoti isadodometse ena. Simuyenera kudya kapena kumwa zakumwa msonkhano uli mkati. (Mlal. 3:1) Yesetsani kuti nthawi zonse muziyang’ana m’bale amene akukamba nkhani. Komanso wokamba nkhaniyo akamawerenga lemba, muzitsegula Baibulo lanu n’kuwerengera naye limodzi. Mungachitenso bwino kulemba notsi zachidule.

4. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azimvetsera ndi kuphunzira?

4 Tikufuna kuti ana athunso azidzamvetsera ndi kuphunzira. Lemba la Miyambo 29:15 limati: “Mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.” Choncho ndi bwino kuti pa msonkhanopo mabanja adzakhale pamodzi kuti makolo aziona ngati ana awo akumvetsera m’malo mosokosera, kulemberana mameseji pafoni kapena kumangoyendayenda. Ngakhale anawo atakhala aang’ono kwambiri moti sangamvetse nkhani zonse zomwe zikukambidwa, akufunikabe kuwaphunzitsa kuti azikhala chete n’kumamvetsera.

5. N’chifukwa chiyani zili zothandiza kubwereza zimene taphunzira ku msonkhano ndipo tingachite bwanji zimenezi?

5 Tsiku Lililonse Pambuyo pa Msonkhano: Muziyesetsa kugona nthawi yabwino kuti mukhale ndi mphamvu tsiku lotsatira. Nthawi zonse zimakhala zothandiza kubwereza zomwe mwaphunzira chifukwa siziiwalika mwamsanga. Choncho tsiku lililonse mukabwerako, pezani nthawi yokambirana ndi banja lanu mfundo zomwe mwamva ku msonkhanoko. Ngati mwapita ku lesitanti madzulo ndi anzanu, mungachite bwino kutenga notsi zanu zimene mwalemba tsikulo n’kukambirana ndi anzanuwo mfundo zimene zakusangalatsani. Msonkhano ukadzatha, mudzakambirane ndi banja lanu pa Kulambira kwa Pabanja mfundo za pa msonkhanowo, n’kuona mmene mungazigwiritsire ntchito m’banja lanu. Komanso mlungu uliwonse, sankhani tsiku limodzi limene muzikambirana mfundo za m’mabuku ndi zinthu zina zatsopano zomwe zinatuluka pa msonkhanowo.

6. Kodi kungopezeka pa msonkhano wachigawo n’kokwanira? Fotokozani.

6 Munthu sanganene kuti anali kuphwando losangalatsa ngati sanadye chilichonse kuphwandoko. N’chimodzimodzinso ndi phwando lauzimu limene Yehova watikonzera pa msonkhano wachigawo. Kuti tidzapindule, tisadzaphonye nkhani iliyonse ya msonkhanowo, tidzamvetsere mwatcheru komanso tidzagwiritse ntchito zimene taphunzirazo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena