Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/01 tsamba 4
  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Tcherani Khutu ku Mawu a Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Mvetserani ndi Kuphunzira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kusonkhana Pamodzi Kuti Titamande Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 7/01 tsamba 4

‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’

1 Buku la Miyambo limasonyeza nzeru ikuitana kuti: “Imvani, pakuti ndikanena zoposa, ndi zolungama potsegula pakamwa panga. Ndine mwini uphungu ndi kudziŵitsa . . . mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga. Pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzam’komera mtima.” (Miy. 8:6, 14, 32, 35) Mawu ameneŵa akufotokoza bwino za malangizo amene tikalandire ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.”

2 Kwaoneka kuti abale padziko lonse ali ndi mavuto, ndipo pulogalamu ya msonkhano wachigawo yakonzedwa kuti tithane ndi mavuto amenewo. Malangizo auzimu ndiponso malingaliro othandiza amene tikamve kumeneko titawagwiritsa ntchito adzatithandiza kukhala achimwemwe, kukhalabe paubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso pamsewu wa kumoyo wosatha. Inde, tili ndi zifukwa zabwino ‘zomvetsera, ndiponso kuwonjezera kuphunzira.’—Miy. 1:5.

3 Pulogalamu Isanayambe: Kuti tipindule kwambiri ndi zimene zikukambidwa, pulogalamu ikamayamba tizikhala tili m’malo athu komanso tili ndi malingaliro abwino. Izi zimalira kulinganiza bwino zinthu. Chinsinsi chake ndicho kuyambirira. Tsiku loti msonkhano ndi maŵa, gonani mofulumira. Dzukani nthaŵi yabwino kuti nonse kwanuko mukhale ndi nthaŵi yokwanira yokonzekera ndiponso yodyera. Fikani msanga kumalo amsonkhano kuti mukapeze malo ndiponso kuti mukasamalire zinthu zofunika pulogalamu isanayambe. Tsiku lililonse mapulogalamu azidzayamba 8:30 a.m.

4 Popeza cholinga cha kusonkhana kwathu ndicho kutamanda Yehova “m’masonkhano,” chigawo chilichonse chizidzayamba mwanjira yolemekeza Mulungu wathu. (Sal. 26:12) N’chifukwa chake, tonse tikulimbikitsidwa kukhala pansi asanalengeze nyimbo yotsegulira. Izi zimagwirizana ndi langizo la m’Malemba lakuti: “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.” (1 Akor. 14:40) Kodi zimenezi zikutanthauzanji kwa aliyense wa ife? Mukaona tcheyamani atakhala papulatifomu nyimbo zamalimba zoyamba zija zili m’kati, khalani pansi mwachangu. Zidzakuthandizani kuimba ndi mtima wonse nyimbo yotsegulira chigawo chilichonse, kutamanda Yehova mokweza.—Sal. 149:1.

5 Pulogalamu Ili M’kati: Ezara“adaikiratu [“anakonzekeretsa,” NW ] mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita.” (Ezara 7:10) Kodi tingakonzekeretse motani mitima yathu kuti tilandire malangizo a Yehova? Popenda mitu imene ili papulogalamu, dzifunseni kuti, “Kodi Yehova akundiuza chiyani pa pulogalamu imeneyi? Kodi ndingagwiritse ntchito motani mfundo zimenezi kuti ndipindule ndi banja langa?’ (Yes. 30:21; Aef. 5:17) Dzifunsenibe mafunso ameneŵa mpaka msonkhano uthe. Lembani mfundo zimene mukufuna kugwiritsa ntchito. Pamapeto a chigawo chilichonse khalani ndi nthaŵi yokambirana zimenezi. Kutero kudzakuthandizani kukumbukira ndi kugwiritsa ntchito mfundozo.

6 Kumvetsera mwatcheru nthaŵi yaitali n’kovuta. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti malingaliro athu asaganize zina? Gwiritsani ntchito mphamvu ya maso. Kaŵirikaŵiri malingaliro athu amakhala pomwe pali maso athu. (Mat. 6:22) Chotero, dziletseni kutembenuka mukamva phokoso lililonse kapena m’gugu. Maso anu azikhala pa wokamba nkhani. Tsatirani m’Baibulo lanu akamaŵerenga lemba, musatseke Baibulo lanu pamene akufotokoza lembalo.

7 Kukonda Akristu anzathu kudzatithandiza kusadodometsa ena pulogalamu ili m’kati. (1  Akor. 13:5) Imeneyi ndi “mphindi yakutonthola” ndi kumvetsera. (Mlal. 3:7) Choncho, peŵani kulankhula kosafunika ndi kuyendayenda. Chepetsani kupitapita kuchimbudzi mwa kukonzekeratu. Musadye kapena kumwa mpaka nthaŵi yake itakwana, pokhapokha ngati muli ndi matenda aakulu. Amene amabwera ndi matelefoni am’manja, zinthu zolira, makamera avidiyo ndiponso makamera asadodometse nazo ena akamazigwiritsa ntchito. Makolo akonze kuti banja lawo lonse ndi achinyamata omwe adzakhale pamodzi kuti adzathe kuwayang’anira bwino.—Miy. 29:15.

8 Chaka chatha mkulu wina amene wakhala akupezeka pamisonkhano yachigawo kwa zaka zambiri anati: “Ndikuona kuti msonkhano uno waposa ina yonse pa chifukwa chimodzi. Pafupifupi aliyense anali kulemba notsi, ndi ana omwe. Zinali zosangalatsa kwambiri. Mabaibulo anagwira ntchito yake wokamba nkhani akapempha kuti aŵerenge mawu ena.” N’kwabwinodi kumvetsera mwatcheru chonchi. Sikuti kutero kumapindulitsa ife ndi opezeka pamsonkhano okha komatu koposa zonse kumalemekeza kwambiri Mphunzitsi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu.—Yes. 30:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena