‘Khalani Owoloŵa Manja, Okonzeka Kugaŵira Ena’
1 Zaka mazana ambiri zapitazo mtumwi Paulo analangiza Timoteo kulimbikitsa okhulupirira anzake “kuti achite zabwino, kukhala ochuluka mu ntchito zabwino, kukhala owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena.” (1 Tim. 6:18, NW) Paulo anakumbutsanso Akristu achihebri kuti asaiŵale “kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena.” (Aheb. 13:16) Kodi analemberanji malangizo ameneŵa? Chifukwa chakuti anadziŵa kuti kukakhala “ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino.”—Aroma 2:10.
2 Chifukwa chakuti ndi Mlengi, Yehova Mulungu ndiye Mwini zonse. (Chiv. 4:11) Timayamikira zimene amatichitira pogwiritsa ntchito zinthu zake. Ngakhale kuti anthu ambiri sayamika, Wam’mwambamwamba akupitiriza kupindulitsa aliyense ndi makonzedwe ake owoloŵa manja ochirikizira moyo. (Mat. 5:45) Anapereka ngakhale Mwana wake wokondedwayo monga nsembe kuti tikapeze moyo wosatha. Kodi chikondi chimene watichitira si chiyenera kutisonkhezera kukhala oyamikira mwa kukhala owoloŵa manja kwa anthu anzathu?—2 Akor. 5:14, 15.
3 Kodi Tingagaŵire Ena Chiyani? N’koyenera kuti tigwiritse ntchito katundu aliyense amene tili naye mwanjira yokondweretsa Mulungu. Ndithudi tifunika kuchirikiza ntchito ya Ufumu yapadziko lonse mwakuthupi ndiponso mwauzimu. N’zoona kuti uthenga wabwino ndicho chuma chamtengo wapatali choposa zina zonse zimene munthu angakhale nazo, popeza “uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu.” (Aroma 1:16) Mwezi uliwonse, mwa kugwiritsa ntchito nthaŵi ndi katundu wathu mowoloŵa manja kuti tichite nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, tingathe kugaŵira ena chuma chauzimu chimenechi, chowatsogolera kupeza moyo wosatha.
4 Yehova amasangalala kwambiri ngati tithandiza anthu opeza movutika. Iye akulonjeza kutidalitsa, ndipo amatikumbutsanso kuti: “Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.” (Miy. 11:4; 19:17) Kuchirikiza ntchito ya Ufumu mwakuthupi ndiponso kulalikira nawo uthenga wabwino mokwanira ndizo njira zabwino kwambiri zosonyezera kuti ndifedi owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena.