“Khalani Ochuluka mu Ntchito Zabwino”
1 Mtumwi Paulo m’zaka zomaliza za utumiki wake wachangu, anagwira ntchito kwambiri ndi Timoteo ndi Tito. Onseŵa anawalembera mawu ofanana owalimbikitsa. Anauza Tito kuti “iwo akukhulupirira Mulungu” afunika ‘kukhalabe atsogoleri a ntchito zabwino.’ (Tito 3:8) Anauza Timoteo kuti anthu odalira Mulungu afunika “kukhala ochuluka mu ntchito zabwino.” (1 Tim. 6:17, 18, NW) Ameneŵa ndi malangizo abwino kwambiri kwa tonse. Koma kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuchita ntchito zabwino m’moyo wathu? Kodi masiku akubweraŵa ndi ntchito ziti zimene tingachite?
2 Chimene chimatilimbikitsa kuchita ntchito zabwino zochuluka ndi kukhulupirira kwathu Yehova ndi kum’konda ndiponso chiyembekezo chabwino chimene watipatsa. (1 Tim. 6:19; Tito 2:11) Makamaka panyengo ino, tikukumbukira kuti Yehova anatumiza Mwana wake, Yesu, padziko lapansi kudzachotsa chitonzo pa Atate ake ndi kudzatsegula njira yakuti anthu oyenera akapeze moyo wosatha. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Zimenezi akazilongosola bwino pa March 28 pa mwambo wokumbukira imfa ya Kristu. Kodi kuyamikira chiyembekezo cha moyo wosatha sikutilimbikitsa kuyesetsa “kukhala ochuluka mu ntchito zabwino”? Ndithudi kumatilimbikitsa. Kodi ndi ntchito ziti zimene tingachite pakalipano?
3 Ntchito Zabwino Zoti Tichite mu March ndi Miyezi Yotsatira: Mosakayikira tidzapita ku Chikumbutso—umene ndi mwambo wapachaka wofunika kwambiri kwa Mboni za Yehova padziko lonse. (Luka 22:19) Koma tikufuna kudzasangalala ndi anthu ambiri pa mwambowu. Taonani lipoti la utumiki mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2002, ndipo muona kuti chaka chatha m’mayiko ambiri padziko lapansi, opezeka pa Chikumbutso anaŵirikiza katatu, kanayi, kasanu kapena kuposerapo chiŵerengero cha ofalitsa. Ndithudi onse mu mpingo anayesetsa kugaŵira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso m’gawo lawo lonse. Choncho, tikufuna kuthera nthaŵi yambiri kuyambira panopo mpaka pa March 28 kuitanira anthu ku Chikumbutso, powathandiza kuphunzira za chipulumutso.
4 Mwezi wa April ukamayamba, mwina tidzakhala titayamba nyengo yabwino. Kodi ndi motani momwe tingagwiritsire ntchito mwanzeru mwayi umenewu kukhala “ochuluka mu ntchito zabwino”? Mwa kugwirabe mwachangu ntchito yolalikira uthenga wabwino, kukhala “achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14; Mat. 24:14) Ngati munalephera kuchita upainiya wothandiza mu March, kodi mungachite mu April ndi May? Ngati mukuchita upainiya mu March, kodi simungapitirize?
5 Anthu ena apantchito amaona kuti popita kuntchito akhoza kulalikira kwa ola limodzi kapena kuposa, kuchita umboni wa mumsewu kapena kulankhula anthu amalonda amene amatsegula m’maŵa kwambiri. Ena amapatula nthaŵi yawo yopuma masana kuti alalikire. Ena panthaŵi imeneyi amaona kuti n’zotheka kuchita phunziro la Baibulo ndi wantchito mnzawo. Alongo ambiri amene sagwira ntchito amapatula nthaŵi ya utumiki wakumunda ana awo ali kusukulu. Masiku ena amadzuka msanga kuti agwiriretu ntchito zapakhomo ndipo masana amakhala ndi nthaŵi yochuluka yogwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa.—Aef. 5:15, 16.
6 Ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza, mungakonze ndandanda yanu kuti muchite zochuluka mu utumiki, kuyesetsa ‘kuchita zabwino, kukhala ochuluka mu ntchito zabwino, kukhala owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena’ choonadi.—1 Tim. 6:18.
7 Osaiŵala Ntchito Yabwino Yopanga Ophunzira: Chaka chilichonse anthu achidwi amabwera ku Chikumbutso. Kodi anthu ena mu mpingo angathandize anthu amene amabwera ku Chikumbutso koma saphunzira ndi wina aliyense? Kodi tingapange maulendo obwereza kwa iwo kukawathandiza kupita patsogolo mwauzimu? N’kutheka kuti ena mwa anthu ameneŵa abale awo ndi Mboni. Ena ndi anthu amene m’mbuyomo anali kuphunzira ndipo akungofunika kuwalimbikitsa kuti ayambirenso kuphunzira ndi kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse. Zingakhaletu zosangalatsa kwambiri anthu ameneŵa atakhala atumiki a Yehova achangu pamodzi ndi ife.
8 Tikachita zochuluka mu utumiki mwezi wa March ndiponso miyezi yotsatira, tidzapeza anthu achidwi ambiri omwe tingawayenderenso. Tiziwasiyira funso, n’kuwauza kuti funsolo tidzayankha ulendo winawo. Tikatere, ndiye kuti talambula njira ya ulendo wobwereza. Ndi bwino kubwererako mwamsanga. Ngati sitinayambitse phunziro paulendo woyamba, paulendo wobwereza tiziyesetsa kuyambitsa phunziro.
9 Polalikira mumsewu, tizichita khama kuyamba kulankhula anthu. Ofalitsa ambiri atenga mayina, maadiresi, ndi manambala a telefoni kwa anthu achidwi amene amakumana nawo mu ulaliki wa mumsewu. Ngati munthuyo sakhala mu gawo lanu, perekani dzina ndi adiresi ya munthuyo kwa mlembi wa mpingo, amene adzatumiza zimenezi ku mpingo wadera limene munthuyo amakhala. Mlembi akalephera kuchita zimenezi, adzatumiza zimenezi ku ofesi ya nthambi kuti achite zimenezi. Mwa njira imeneyi, tingakulitse chidwi chawo.
10 Ngati tatenga nambala ya telefoni yokha popanda adiresi, chitani ulendo wobwereza mwa kumuimbira munthuyo telefoni. Konzekeranitu zimene mukufuna kukambirana. Buku lanu la Kukambitsirana lizikhala pafupi kuti muzitha kuona mosavuta. Ena zikuwayendera bwino pophunzira ndi anthu patelefoni komanso ndi amene amavuta kuwapeza pakhomo. Mlongo wina ankafunsa amayi achidwi amene anakumana nawo mu utumiki wa khomo ndi khomo manambala awo a telefoni, ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo aŵiri.
11 Mverani Akulu Pothandiza Osagwira Ntchito: Akulu amakonda kwambiri kuthandiza anthu ameneŵa. Ena mwa anthu ameneŵa anayambanso okha kupezeka pamisonkhano ya mpingo. Amadziŵa kuti n’kofunika kukhala m’gulu la Yehova kuti apeze chitetezo chauzimu chotchulidwa pa Salmo 91. Ena a iwo ndi okonzeka tsopano kuyambiranso kuloŵa mu utumiki wakumunda. Ngati enanso osagwira ntchito adzabwera pa Chikumbutso mwezi uno, mwina adzalola kuphunzira nawo Baibulo. Zikatere, akulu adzakonza zoti wina aziphunzira ndi amene akufuna thandizo. Akakupemphani kuti muthandize mwa njira imeneyi, adzayamikira kwambiri mukavomera.—Aroma 15:1, 2.
12 Pitirizani “Kuchita Ntchito Zabwino”: Anthu ambiri amene achita utumiki waupainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo apeza kuti amachita zambiri mu utumiki wakumunda m’miyezi yotsatira. Anakumana ndi anthu achidwi omwe anafunika kuwayenderanso. Zimenezi zinawalimbikitsa kuyesetsa kupita pafupipafupi mu utumiki wakumunda kuti akafikenso kwa anthu achidwiwo. Ena anayamba maphunziro, ndipo zimenezo zinawathandiza kuchita zochuluka kwambiri mu utumiki.
13 Komanso ena asangalala kwambiri pochita zochuluka mu ntchito yolalikira ndi yopanga ophunzira moti zawalimbikitsa kupendanso zochita zawo. Chotero, ena anapungula ntchito imene amagwira kuti ayambe kuchita upainiya wothandiza mosalekeza. Ena ayamba utumiki wa upainiya wokhazikika. Anadalira kwambiri Mulungu osati zinthu za dziko. Anaona kuti kukhala “owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena,” kunabweretsa madalitso a Yehova ndipo kunalimbitsa chiyembekezo chawo cha “moyo weniweniwo.” (1 Tim. 6:18, 19, NW) Inde, mpingo wonse umapindula ena akayamba utumiki waupainiya. Apainiya amakonda kunena zimene akumana nazo mu utumiki ndipo amapempha anthu ena kuyenda nawo limodzi, ndipo izi zimalimbikitsa mpingo kukonda zauzimu.
14 Tonse ‘tikhale ochuluka mu ntchito zabwino’ panyengo ya Chikumbutso ino ndiponso miyezi yotsatira mwa kuwonjezera zimene timachita mu utumiki wachikristu. Tiyeni tiyamikire zimene Yehova wachita potipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha mu dziko lapansi latsopano lolungama.—2 Pet. 3:13.