‘Chitirani Onse Chokoma’
1 “Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu” ndiponso “Khalani Ochuluka mu Ntchito Zabwino” inali mitu ya nkhani m’mphatika za Utumiki Wathu wa Ufumu wa February ndi wa March, 2002. (Akol. 1:25; 1 Tim. 6:18) M’makope ameneŵa tinalimbikitsidwa kuti tiyesetse kuthandiza anthu achidwi kupezeka pa Chikumbutso, kuthandiza anthu osagwira ntchito kuyambiranso kugwirizana ndi mpingo, ndiponso kuthandiza ana athu ndi ophunzira Baibulo oyenerera kuyamba kulalikira uthenga wabwino. Tikukhulupirira kuti tapindula nalo khama lathu. Tsopano ‘monga tili nayo nyengo, [tipitirize] kuchitira onse chokoma.’—Agal. 6:10.
2 Apempheni Kuti Adzabwerenso: Chaka chilichonse ku Malaŵi kuno, pa Chikumbutso pamabwera anthu oposa 100,000 amene si ofalitsa uthenga wabwino. Popeza kubwera kwawo kumasonyeza kuti ali ndi chidwi, kodi tingatani kuti tiwalimbikitse anthu “ofuna moyo wosatha” kukhala “okhulupirira”? (Mac. 13:48, NW) Alimbikitseni kuyamba msanga kupezeka pa misonkhano ya mpingo.
3 Bwanji osapempha munthu wachidwi kudzakhala nanu pa Phunziro la Buku la Mpingo kuti naye adzasangalale ndi makambirano abwino a ulosi wa Yesaya? Ngati ndinu wachibale kapena mnzake wa munthu ameneyu ndipo mwapatsidwa nkhani mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase, mungamuitane kuti adzamvere nawo nkhaniyo. M’dziŵitseni mitu ya nkhani za onse zimene zikambidwe milungu ikudzayo. (Ndandanda ya nkhanizo ili pabolodi la chidziŵitso.) Pezani njira imene mungam’limbikitsire kulambira Yehova. Ndipo ngati sanayambebe kuphunzira Baibulo ndi munthu wina mumpingowo, m’pempheni kuti muziphunzira naye.
4 Pitirizani Kulimbikitsa Anthu Osagwira Ntchito: Ena amene anafika pa Chikumbutso anadzipatulira kale kwa Yehova. Komabe, nthaŵi ina analeka kulalikira mwachangu uthenga wabwino. Paulo akutilimbikitsa kuti ‘tichitire chokoma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.’ (Agal. 6:10.) Choncho, tiyenera kuthandiza kaye anthu osagwira ntchito.
5 Mwina ena ayambanso kuloŵa mu utumiki chifukwa chakuti akulu ndiponso anthu ena anawalimbikitsa. Ngati akulu akupemphani kuti muyende ndi wofalitsa amene wayambanso kugwira ntchito, dziŵani kuti kukonda kwanu Yehova ndi utumiki wa kumunda kudzalimbikitsa wofalitsayo. Muonetseni momwe mumachitira mitundu yosiyanasiyana ya utumiki kuti naye azisangalala kuchita zimenezo, apitirize ntchito yolalikira ndiponso apeze madalitso a Yehova.
6 Athandizeni Ofalitsa Atsopano Kuuyamba Bwino Utumiki Wawo: Mkazi wina atangosonyeza chidwi kumene n’kuona kuti wapeza gulu loona la Mulungu, anafuna kuyamba kuloŵa mu utumiki nthaŵi yomweyo. Ataphunzira zimene anafunika kuti achite, anati: “Ndikufuna ndiyambe nthaŵi yomwe ino.” Ngati munthu amene mwakhala mukuphunzira naye Baibulo wavomerezedwa kuyamba kuloŵa mu utumiki wa kumunda, m’thandizeni kuona kufunika ‘koyamba nthaŵi yomweyo,’ ndipo m’thandizeni wofalitsa watsopanoyo kuuyamba bwino utumiki wake. M’thandizeni kuti azoloŵere kukonzekera ndiponso kuloŵa nawo mu utumiki wa kumunda mlungu uliwonse.
7 Ngati wofalitsa watsopano wosabatizidwayo ndi mwana wanu, yendani naye mu utumiki kuti apite patsogolo malinga ndi msinkhu wake ndi luso lake. Mukamuthandiza pang’ono chabe, mudzadabwa momwe akuchitira bwino pokambirana ndi anthu, kuŵerenga Baibulo ndi kugaŵira magazini. Akapeza munthu wachidwi mu utumiki wa kumunda, m’phunzitseni kupitakonso kukakulitsa chidwi cha munthuyo.
8 Onjezerani Utumiki Wanu: Kodi moyo wanu ukukupatsani mpata wowonjezera ntchito yanu yolalikira ngakhale nyengo ya Chikumbutso itatha? Kodi mungawonjezere ola limodzi kapena aŵiri pa maola amene mumathera mu utumiki mlungu uliwonse? Kodi mukuyembekezera mwachidwi nthaŵi imene mudzachitenso upainiya wothandiza? Kapena kodi mungasinthe zochita zanu kuti muyambe utumiki wa nthaŵi zonse? Zimene timachita mu utumiki zingathandize munthu wina kuphunzira choonadi. (Mac. 8:26-39) Pamene tikudikira za m’tsogolo, tiyeni ‘nthaŵi zonse titsatire chokoma, kwa anzathu, ndi kwa onse.’—1 Ates. 5:15.
[Bokosi patsamba 3]
Pitirizani Kuthandiza:
□✔ Opezeka pa Chikumbutso
□✔ Ofalitsa oyambanso kugwira ntchito
□✔ Ofalitsa atsopano osabatizidwa