Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/00 tsamba 1
  • “Muchite Zonse Kukumangirira”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Muchite Zonse Kukumangirira”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzindikira Kukuchinjirizeni
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Bizinesi Yanu Idzakutayitsani Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khalani Womangirira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Musasiye Okhulupirira Anzanu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 7/00 tsamba 1

“Muchite Zonse Kukumangirira”

1 Pochita zinthu ndi abale athu, tiyenera kuwachitira zabwino zowamangirira. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kukhala wofunitsitsa kutchinjiriza zinthu zawo zauzimu. Ngati timachita ntchito ina yake yakuthupi imene imaphatikizapo kutsatsa malonda, tiyenera kusamala kuti tisachite chilichonse chimene chidzakhumudwitsa abale athu.—2 Akor. 6:3; Afil. 1:9, 10.

2 Ena aloŵa m’malonda osiyanasiyana, akumaona Akristu anzawo kukhala makasitomala. Mabungwe ena ogulitsa zinthu amalimbikitsa anthu owaimira kuti aziona aliyense kukhala kasitomala—kuphatikizapo anthu a m’chipembedzo chawo. Abale ena akonza misonkhano ikuluikulu ya Mboni n’cholinga chowalimbikitsa kuti aloŵe nawo m’malonda. Ena amachirikiza malonda awo mwa kufalitsa nkhani zopeka, mabulosha, nkhani za pa intaneti, kapena makaseti avidiyo ndi makaseti wamba kwa okhulupirira anzawo. Kodi kungakhale koyenera kuti Mkristu agwiritse ntchito maunansi ake ateokalase, kudyera masuku pamutu abale ake auzimu? Ayi!—1 Akor. 10:23, 24, 31-33.

3 Abale Ayenera Kusamala: Izi sizikutanthauza kuti Mkristu sangachite malonda ndi mbale. Imeneyi ndi nkhani yaumwini. Komabe, ena amayambitsa malonda amene amachirikiza dyera, ndipo amalimbikitsa okhulupirira anzawo kuti achitire limodzi malondawo kapena awaikize ndalama. Ambiri a malonda ameneŵa amakanika, akumaloŵetsa m’madzi ndalama zambiri za anthu amene anachita nawo. Ngakhale kuti amene analoŵa nawo m’malondayo angakhale atasonkhezeredwa ndi chikhumbo chofuna kupeza ndalama mwachangu, woyambitsa malondayo sayenera kuganiza kuti alibe mlandu ngati malondawo akanika. Ayenera kupenderatu mmene umoyo wauzimu ndi wakuthupi wa abale akewo udzakhalire ngati malondawo atati asaphule kanthu. Makamaka amene ali ndi maudindo ateokalase ayenera kukhala osamala ndi malonda awo chifukwa ena amawalemekeza ndiponso kuwakhulupirira kwambiri. Kukakhala kulakwa kusagwiritsa ntchito bwino chikhulupiriro chimenechi. Mbale angataye maudindo a utumiki wopatulika ngati ena sam’lemekeza.

4 Cholinga chathu chiyenera kukhala ‘kuchita zonse kukumangirira.’ (1 Akor. 14:26) Tiyenera kupeŵa kuchita chilichonse chimene chidzayambitsa kapena kuchirikiza malonda mumpingo. Zinthu zimenezi si ndizo zifukwa zathu za m’Malemba zomwe timasonkhanira pamodzi.—Aheb. 10:24, 25.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena