Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira July 10
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Thirirani ndemanga pa lipoti la utumiki wakumunda la April la dziko lino ndi la mpingowo. Pendani zili m’bokosi lakuti “Onani Tsamba Lomaliza,” ndipo onetsani chitsanzo chimodzi mwa maulaliki operekedwawo omwe angagwire ntchito mogwira mtima m’gawo lanu.
Mph. 15: “Sitingathe Ife Kuleka Kulankhula.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosapitirira imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani chifukwa chake sitiona ntchito yathu yolalikira mwachibwanabwana. Phatikizanipo mfundo zogwirizana ndi nkhaniyi zopezeka mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1997, masamba 23-4.
Mph. 18: “Muchite Zonse Kukumangirira.” Akulu aŵiri akambirane nkhaniyi. Agogomezere kufunika kwa kuzindikira pankhani za malonda kapena kuikiza ndalama. Onaninso uphungu wopezeka mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1997, masamba 18-19, 22.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 17
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Fotokozani mwachidule mmene tingagwiritsire ntchito bulosha la Dzina la Mulungu pothandiza munthu wachidwi kuzindikira kufunika kodziŵa ndiponso kogwiritsa ntchito dzina lake la Mulungu.—Onani buku la Kukambitsirana, masamba 420-1.
Mph. 10: “Kodi Muli ndi Oda Yokhazikika ya Magazini?” Kambiranani ndi kupendera limodzi ndi omvetsera. Pemphani ena kusimba mmene adzatsatirire chilimbikitso chimene chaperekedwacho.
Mph. 20: “Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Gogomezerani kufunika kopezeka pamsonkhano wachigawo masiku onse atatu.
Nyimbo Na. 34 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 24
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Tcherani Khutu ku Mawu a Mulungu.” Mafunso ndi mayankho. Gogomezerani chifukwa chake tonsefe tiyenera kukhala m’malo mwathu chigawo chilichonse chikamayamba, kumvetsera mwatcheru ndiponso kusadodometsa ena.
Mph. 15: “Khalani ndi Khalidwe Labwino Limene Limalemekeza Mulungu.” Mkulu akambirane nkhaniyi ndi banja. Apende zimene afunika kuchita kuti akhale chete, akhalidwe labwino, audongo, ndi opereka chitsanzo chabwino m’maonekedwe ndiponso m’zochita zawo m’malo ena akapita kumsonkhano.
Mph. 10: Gwiritsani Ntchito Mawu Oyamba Ogwira Mtima. Sankhani mawu oyamba patsamba 9–15 m’buku la Kukambitsirana, ndiyeno kambiranani mmene mawuwo angagwiritsidwire ntchito mogwira mtima m’gawolo. Funsani omvetsera kuti “Kodi mumayamba bwanji kulankhulana ndi munthu pamsewu, mwamwayi, ndi m’maulaliki ena?” Ngati nthaŵi ilola, sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri cha mmene tingayambire.
Nyimbo Na. 54 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 31
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a July. Perekani ndemanga pa nkhani yakuti “Kuphunzira Ulosi wa Danieli!” Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zimene asangalala nazo mwezi uno pogaŵira mabulosha.
Mph. 12: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: “Kodi Mumayamikira Kuleza Mtima kwa Yehova?” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zogwirizana ndi kuleza mtima kwa Yehova.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 17: “Kodi Ndinu Munthu Wamanyazi?” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 18: Khalani Wanzeru ndi Tsogolo Lanu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Achinyamata amafuna kusangalala ndi tsogolo lachimwemwe pamodzi ndi okondedwa awo. Ngakhale kuti ichi n’chibadwa, ayenera kugwiritsa ntchito uphungu wa Mulungu ngati akufuna kupindula. (Miy. 19:20) Chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu mwa achinyamata. Ngati malingaliro amenewo saletsedwa, zotsatira zake zingakhale zovulaza. Pamakhala mafunso ambiri ngati n’kwanzeru kuti achinyamata azikondana ndi munthu wosiyana naye ziwalo, kukhala ndi chilakolako cha kugonana chimene chimatsogolera kuchita chibwenzi. Pendani malangizo operekedwa mu buku la Achichepere Akufunsa, masamba 231-5. Gogomezerani mfundo zazikulu za mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1999, masamba 18-23, amene amasonyeza kufunika kwa achinyamata kukwaniritsa udindo wawo wonse kwa Mulungu. Limbikitsani anyamata kulingalira za uphungu umenewu ndiponso kuti akakambirane ndi makolo awo ngati ali ndi mafunso.
Nyimbo Na. 101 ndi pemphero lomaliza.