Gwiritsani Ntchito Nkhani Zochitika Zaposachedwapa Kuti Mudzutse Chidwi
1 Kodi mukufuna malingaliro abwino owonjezereka amene adzachititsa utumiki wanu kukhala watsopano ndiponso wodzutsa anthu chidwi cha uthenga wa Baibulo? Ndiye gwiritsani ntchito nkhani zimene zikuchitika m’dziko ndi m’dera lanu kuyambitsira zokambirana. Mungakambe nkhani zochitika zaposachedwapa za m’deralo ndi m’dzikolo kapena za m’mayiko osiyanasiyana. Nkhani zimenezi zimasinthasintha. (1 Akor. 7:31) Onani zitsanzo zotsatirazi.
2 Mavuto a zachuma ndi kukwera mitengo kwa zinthu ndizo zimadetsa nkhawa kwambiri anthu. Choncho, munganene kuti:
◼ “Kodi munamva pankhani kuti [tchulani chinthucho] chakweranso mtengo?” Kapena mukhoza kuthirira ndemanga pa ulova ngati kampani inayake yachotsa ntchito anthu ambiri. Malinga ndi mmene mukufunira kupitirizira kukambiranako, mukhoza kupitiriza mwa kufunsa funso ili “Kodi munayamba mwafunsapo chifukwa chake kuli kovuta kwambiri kupeza zofunika pamoyo?” kapena mungafunse kuti “Kodi muganiza kuti kupeza zofunika pamoyo kudzakhala kovuta mpaka kalekale?”
3 Nkhani za chiwawa, monga mavuto m’banja kapena chiwawa cha ana asukulu, zili zina zomwe tingagwiritse ntchito kuyambitsira kukambirana. Mungafunse kuti:
◼ “Kodi munaŵerenga mu nyuzipepala kuti [tchulani vuto la m’deralo]?” Ndiyeno funsani funso ili “Kodi muganiza kuti n’chiyani chimachititsa chiwawa chochuluka chonchi m’dziko?” kapena funsani kuti “Kodi muganiza kuti idzafika nthaŵi imene tidzakhala otetezeka?”
4 Nkhani za kusefukira kwa madzi, zivomezi, kapena nkhondo zapachiŵeniŵeni m’mayiko osiyanasiyana zimakhalanso zodzutsa chidwi. Mwachitsanzo, mungafunse kuti:
◼ “Kodi Mulungu ndiye amene amachititsa [tchulani tsoka lachilengedwe]?” Kapena mutha kukamba za nkhondo yapachiŵeniŵeni imene ikuchitika ndipo nenani kuti: “Ngati aliyense amafuna mtendere, n’chifukwa chiyani uli wovuta kwambiri kuupeza?”
5 Khalani tcheru kuti mumve nkhani zimene zachitika posachedwapa zomwe mungagwiritse ntchito m’mawu anu oyamba. Malangizo othandiza akupezeka m’buku la Kukambitsirana, patsamba 14, pamutu wakuti “Zochitika Zatsopano.” Komabe, peŵani kuloŵerera m’zandale kapena m’nkhani za kakhalidwe ka anthu. M’malo mwake, kambani za Malemba ndi Ufumu wa Mulungu monga chida chokha chimene chingathetse mavuto amtundu wa anthu.