Kulalikira M’dziko Losinthasinthali
1 Zinthu sizichedwa kusintha. Mwadzidzidzi, nkhani ya tsoka lachilengedwe, mavuto a zachuma, a zandale, kapena nkhani ya tsoka limene lafalitsidwa kwambiri ingakhale ili mkamwamkamwa. Komanso, anthu sangachedwe kuika maganizo pa zinthu zina. (Mac. 17:21; 1 Akor. 7:31) M’dziko losinthasinthali, kodi tingatani kuti tichititse anthu kumvetsera uthenga wa Ufumu umene tikuwauza?
2 Dziŵani Zimene Zikuwadetsa Nkhaŵa: Kutchula nkhani zimene zangochitika kumene ndi njira imodzi imene tingachititsire anthu kumvetsera. Nthaŵi ina Yesu polimbikitsa omvera ake kuganizira mofatsa kukhulupirira kwawo Mulungu, anatchula masoka amene anachitika kumene, amene anali m’maganizo mwa anthuwo. (Luka 13:1-5) Mofananamo, polalikira uthenga wabwino, ndi bwino kugwirizanitsa ulalikiwo ndi nkhani zimene zachitika posachedwa kapena nkhani ya m’deralo imene yawakhudza mtima anthu a m’gawo lathu. Komabe, pokambirana nkhani zoterezo, tizisamala kuti tisasonyeze kuloŵerera m’nkhani zandale kapena zokhudza zochita za anthu.—Yoh. 17:16.
3 Kodi tingadziŵe bwanji zimene anthu akuganiza panthaŵiyo? Mwina njira yabwino yodziŵira zimenezi ndi kungofunsa funso ndi kumvetsera zimene ayankhe. (Mat. 12:34) Kuchita chidwi ndi anthu kudzatilimbikitsa kudziŵa maganizo a anthu ena ndiponso kufunsa mwaluso kuti timve zambiri. Yankho lochokera mumtima la mwininyumba lingasonyeze vuto la anthu ambiri m’deralo ndipo zingapereke mpata wolalikira.
4 Kukonzekera Ulaliki: Pokonzekera utumiki wakumunda m’dziko losinthasinthali, tingagwiritse ntchito buku la Kukambitsirana. Mfundo zothandiza zosonyeza mmene tingagwirizanitsire nkhani zimene zachitika posachedwa ndi ulaliki wathu zili patsamba 14, pamutu wakuti “Upandu/Chisungiko” ndi “Zochitika Zatsopano.” Pokonzekera ulaliki wanu, yesetsani kuphatikizapo lemba logwirizana ndi nkhaniyo.
5 Tikamaganizira mavuto amene amasinthasintha a anthu a m’gawo lathu, tiyenera kugwirizanitsa zimenezi ndi ulaliki wathu wa uthenga wabwino. Tikatero, tidzakambirana ndi anthu zimene zimakhudza kwambiri moyo wawo. Chotero, tidzathandiza anthu ambiri kudziŵa Mulungu amene sasintha makhalidwe ake ndi miyezo yake.—Yak. 1:17.