“Mawu Oyenera a pa Nthaŵi Yake”
1 Kodi kuuza ena uthenga wa moyo kumakhala kovuta kwa inu? Kodi mumaona kuti muyenera kunena mawu ozama kuti mukope omvera anu? Pamene Yesu anatumiza ophunzira ake, anawauza kuti: “Lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mat. 10:7) Uthengawo unali wapafupi komanso wosavuta kuuza ena. Leronso ndi chimodzimodzi.
2 Kaŵirikaŵiri, mawu ochepa okha amatha kuyambitsa makambirano. Filipo atakumana ndi mdindo wa ku Aitiopiya, anam’funsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” (Mac. 8:30) Si kupindulitsa kwake makambirano amene anatsatirapo, ochokera mu “mawu oyenera a pa nthaŵi yake”!—Miy. 25:11.
3 Inunso mutha kugwiritsa ntchito njira yofananayo mu ulaliki wanu. Motani? Mwa kukhala wozindikira ndi kusankha mawu oyenerera mkhalidwewo. Funsani funso, kenako mvetserani yankho lake.
4 Ena a Mafunso Osavuta: Pofuna kuyambitsa makambirano, mungayese lililonse la mafunso aŵa:
◼ “Kodi mumapemphera Pemphero la Ambuye (kapena, lakuti Atate Wathu Wakumwamba) pakulambira kwanu?” (Mat. 6:9, 10) Bwerezani mawu ena a pempherolo, kenako nenani kuti: “Anthu ena amafunsa kuti, ‘Kodi dzina la Mulungu limene Yesu akuti liyeretsedwe ndilo dzina liti?’ Enanso amafunsa kuti, ‘Kodi ndi Ufumu uti umene Yesu akunena kuti tiupempherere?’ Kodi mwapeza mayankho okhutiritsa pa mafunso ameneŵa?”
◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti: ‘Cholinga chenicheni cha moyo n’chiyani?’” Fotokozani kuti yankho lake limafuna kum’dziŵa Mulungu.—Mlal. 12:13; Yoh. 17:3.
◼ “Kodi muganiza kuti panthaŵi inayake imfa ingadzachotsedwe?” Gwiritsani ntchito Yesaya 25:8 ndi Chivumbulutso 21:4 kuti mupereke yankho lodalirika.
◼ “Kodi ilipo njira yosavuta yothetsera zipwirikiti za padziko”? Fotokozani kuti Mulungu amaphunzitsa kuti “uzikonda mnzako.”—Mat. 22:39.
◼ “Kodi tsiku lina dziko lapansi lidzawonongedwa ndi tsoka linalake lachilengedwe?” Fotokozani lonjezo la Baibulo lakuti dziko lapansi lidzakhalapo kwamuyaya.—Sal. 104:5.
5 Lalikirani uthenga wabwino m’njira yosavuta, yachindunji komanso mwachifundo. Yehova adzadalitsa khama lanu pouza ena ngakhale “mawu” amodzi okha a choonadi.