Chitani Ntchito Mosangalala
1 Yesu anati monga m’tsiku la Nowa, panthaŵi ya kukhalapo kwake, anthu ambiri ‘sadzadziŵa kanthu.’ (Mat. 24:37-39) Chotero, timadziŵa kuti anthu ambiri sadzalabadira uthenga wabwino wa Ufumu. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achimwemwe pochita utumiki wathu?—Sal. 100:2.
2 Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti uthenga wathu ndi ntchito yathu yolalikira ndi za Mulungu. Kwenikweni kukana kwa aliyense kumvetsera mu utumiki mosasamala kanthu za khama lathu n’kukana Yehova. Kukumbukira kuti Yehova amakondwera ndi kukhulupirika kwathu mu ulaliki kudzatithandiza kukhalabe ndi mtima wosangalala monga ochita mawu a Mulungu.—Yak. 1:25.
3 Chachiŵiri, akadalipo anthu amene adzalandira njira ya Yehova ya chipulumutso. Ngakhale kuti ambiri angakhale amphwayi, adakalipo anthu onga nkhosa ofunika kuwasonkhanitsa pakalipanopa, m’kati mwenimweni mwa masiku otsiriza. Tiyenera kupitiriza kulalikira, kupita “m’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi” n’cholinga ‘chokafunsitsa amene ali woyenera momwemo.’—Mat. 10:11-13.
4 Khalani ndi Maganizo Abwino: Mbiri yoipa ya chipembedzo chonyenga yakhumudwitsa anthu ena. Ena ‘akambululudwa ndi kumwazikana’ chifukwa cha dongosolo lino la zinthu. (Mat. 9:36) Ambiri akudera nkhaŵa chifukwa cha kusoŵa kwawo ntchito, moyo wathanzi, ndi chitetezo. Kuzindikira izi kudzatithandiza kulimbikira ntchito yathu. Yesetsani kuyambitsa nkhani zimene zimadetsa nkhaŵa kwambiri anthu m’dera lathu. Athandizeni kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo wokha udzathetsa zimenezi. Gwiritsani ntchito Malemba ndi mfundo zolunjika m’zofalitsa kuwafika pamtima ndi uthenga wabwino.—Aheb. 4:12.
5 Nthaŵi zonse ife ochita mawu a Mulungu mosangalala tikumbukire kuti: “Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu [yathu].” (Neh. 8:10) Palibe chifukwa chotayira chimwemwe chathu. “Ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.” (Mat. 10:13) Yehova amawonjezera chimwemwe chathu ndiponso mphamvu pamene tipirira moleza mtima mu utumiki wake wopatulika, ndipo amadalitsa kukhulupirika kwathu.