Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/01 tsamba 3
  • Misonkhano Yachigawo—Nthaŵi Yosangalala!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yachigawo—Nthaŵi Yosangalala!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amasonkhanitsa Anthu Ake Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 7/01 tsamba 3

Misonkhano Yachigawo—Nthaŵi Yosangalala!

1 Misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova imakhala nthaŵi yosangalala kwambiri. Kwa zaka zoposa 100, misonkhano imeneyi yathandiza kuchulukitsa anthu m’gulu lathu. Kuyambira tili kagulu kochepa, taona Yehova akudalitsa kwambiri ntchito yathu yapadziko lonse. M’nthaŵi zathu zamakono zino, pamsonkhano wathu woyamba mu 1893, ku Chicago, Illinois, panali anthu 360 ndipo amene anasonyeza kudzipereka kwa Yehova mwa kubatizidwa anali 70. Pamisonkhano Yachigawo yachaka chatha yakuti “Akuchita Mawu a Mulungu” anthu onse pamodzi analipo okwana 9,454,055, obatizidwa anali okwanira 129,367. Zimenezi n’zosangalatsa kwambiri!

2 Kuyambira mu nthaŵi za m’Baibulo, misonkhano ya anthu a Mulungu yakhala njira yaikulu yolandirira malangizo a Yehova. Mu nthaŵi ya Ezara ndi Nehemiya, anthu anali kumvetsera Chilamulo chikuŵerengedwa “kuyambira mbanda kucha kufikira msana.” (Neh. 8:2, 3) Chifukwa chakuti panthaŵiyo anamvetsetsa Chilamulo, anthu ‘anasekerera kwakukulu.’ (Neh. 8:8, 12) Ifenso timasangalala kuti misonkhano yachigawo imatipatsa mpata wabwino wolandira malangizo abwino ndi chakudya chauzimu cha “panthaŵi yake” chimene Yehova amatipatsa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Popeza Yesu anati munthu amakhala ndi moyo “ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu,” misonkhano yachigawo ili yofunika pamoyo wathu wauzimu.—Mat. 4:4.

3 Mpake Kuyesetsa Kukapezekapo: Tonsefe chikhale cholinga chathu kukapezeka pa Msonkhano wonse Wachigawo wachaka chino wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Tikonze zofika mofulumira tsiku lililonse komanso kusachoka kufikira titanena nawo “Amen!” pa pemphero lomaliza. Kuti zimenezi zitheke tisinthe ndandanda ya zochita zathu. Kutsanzika kuntchito kuti mudzapite kumsonkhano wachigawo kungakhale kovutirapo. Tiyenera kulimbikira kupempha, osangoti momwe zidzakhalire m’momwemo. Ngati tidzafune malo ogona kapena zoyendera, tikonzeretu zimenezi mwamsanga. Zilizonse zimene tingayesetse kuchita mpake kutero!

4 Anthu a Yehova amaona kuti madalitso amene amapeza pamsonkhano wachigawo amaposa ndalama. Onani zina mwa zitsanzo za anthu amene anatsimikiza mtima kupezeka pa Msonkhano Wamayiko wa Mboni za Yehova wa 1958 wakuti Chifuno cha Mulungu umene unachitikira ku New York City. Mbale wina anatseka bizinesi yake yomanga kwa masabata aŵiri kuti akathandize komanso kuti akapezeke pamsonkhano. Mbale wina ku zilumba za Virgin anagulitsa malo a maekala asanu kuti banja lake lonse la anthu asanu ndi mmodzi likapezekepo. Banja lachinyamata linagulitsa bwato lawo la injini kuti ana awo atatu onse kuyambira wa miyezi iŵiri mpaka zaka zisanu ndi ziŵiri apite kumsonkhano. Abale atatu apachibale ku California, United States of America, anauzidwa kuti ngati atadzajomba kuntchito, ntchitonso idzathera pomwepo. Komabe zimenezi sizinawalepheretse kupita kumsonkhano wosaiŵalikawo.

5 Yehova Amadalitsa Kuyesetsa Kwathu: Yehova amaona ndiponso amadalitsa khama la anthu ake. (Aheb. 6:10) Mwachitsanzo, pa Msonkhano wa 1950 wakuti Kuwonjezeka kwa Teokalase, panali nkhani yapadera yakuti “Dongosolo Latsopano la Zinthu.” Mbale Frederick Franz anadzutsa chidwi cha anthu onse mwa kufunsa kuti: “Kodi nonsenu mukusangalala kuti pamsonkhano wamayiko uno tili ndi anthu amene adzakhale akalonga a dziko lapansi latsopano?” Kwa zaka zoposa 50 tsopano, tikusangalalabe ndi mmene anafotokozera momveka Salmo 45:16.

6 Titapita kumsonkhano wachigawo wachaka chatha, mutu wa banja lina woyamikira unalemba kalata iyi: “Abale, simungathe kudziŵa miyoyo imene msonkhano uno wapulumutsa. Banja langa linasamukira ku mzinda wina chifukwa cha ntchito, mapeto ake moyo wathu wauzimu unaloŵa pansi. . . Tinanyalanyaza maudindo athu achikristu. Tinasiyanso kupita kumisonkhano ndiponso ku utumiki wakumunda. . . Msonkhano umenewu watilimbikitsa, ndipo tayambanso kukhala ndi zolinga zauzimu ndi kukonzekera kuzikwanitsa.”

7 Yehova akutipatsa chakudya chauzimu chimene timafunikira. Amayala gome la chakudya chamwana alirenji pa misonkhano yathu yachigawo. Kuyamikira kwathu makonzedwe ameneŵa kukutisonkhezera kunena mawu amene Korneliyo ananena kutabwera mtumwi Petro kuti: “Tili tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.” (Mac. 10:33) Chikhale cholinga chathu kupezeka “pamaso pa Mulungu” m’zigawo zonse za Msonkhano Wachigawo wachaka chino wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” ndi kusangalala nawo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena