Konzekerani Kuphunzira Ulosi wa Yesaya!
1 “Olambira okhulupirika angakhale ndi chidaliro kuti Yehova . . . sadzalola kuti dziko la Satana likhalepobe kwa tsiku lina limodzi kupitirira pamene chilungamo chimafuna.” Ameneŵa ndi mawu olimbikitsa kwambiri. Kodi mawuŵa atengedwa kuti? Mu buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1. Kodi ulosi wa Yesaya ukutipatsa zifukwa zokhulupirira mawu olimbikitsawa? Inde, m’buku la m’Baibulo limeneli, nkhani ya chipulumutso yagogomezeredwa mwamphamvu ndiponso momveka. (Yes. 25:9) N’chifukwa chake tidzalimbikitsidwa kwambiri kuphunzira mbali imeneyi ya Mawu a Mulungu pa Phunziro la Buku la Mpingo. Kodi tidzapindula nawo mwa kupezekapo mlungu uliwonse? Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezo?
2 Pa Yesaya 30:20, NW, Yehova amatchedwa ‘Mlangizi wathu Wamkulu.’ Mkristu aliyense ayenera kumvetsera kwambiri pamene Yehova akutilankhula kudzera m’Mawu ake ndiponso m’mabuku onena za m’Baibulo omwe “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa. (Mat. 24:45; Yes. 48:17, 18) Ndi mmene lilili buku la Ulosi wa Yesaya 1. Kodi pophunzira bukuli mungapindule motani zochuluka?
3 Konzekerani Kuyankha: Mlungu uliwonse patulani nthaŵi yokwanira yokonzekera phunziro la buku. Ŵerengani ndime zonse zimene mukaphunzire. Lingalirani mofatsa mafunso operekedwawo. M’buku lanu ikani chizindikiro pamene pali mayankho. Mavesi amene agwira mawu a Yesaya alembedwa m’zilembo zakuda kwambiri. Aŵerengeni mofatsa. Malemba ena onse amene angoikidwapo, aŵerengeni kuti muone kugwirizana kwake ndi nkhani imene mukuphunzira. Sinkhasinkhani zimene mukuphunzira. Ndiyeno ku phunziro lanu la buku katulutseni zimene munapeza pokonzekera.
4 Mbale amene amachititsa phunziro la buku athandize opezeka paphunzirolo kugwiritsa ntchito Baibulo ndiponso kuzindikira kufunika kwa zimene akuphunzirazo. Ngati ndinu woyamba kuyankha funso pandime, yankhani mwachidule ndiponso mosapita m’mbali. Ngati wina wachita kale zimenezi, mungawonjezere pamfundo imene mukukambirana. Mukhoza kufotokoza kugwirizana kwa lemba lofunika kwambiri pandimeyo ndi mutu umene mukuphunzira. Yesetsani kuyankha m’mawu anuanu, ndipo sangalalani mwa kutenga mbali m’makambiranowo.
5 Tonse pamodzi tipende mwachidwi uthenga wapadera mu buku la Yesaya. Udzatilimbikitsa kuti tikhale osangalala tsiku lililonse poyembekeza chipulumutso cha Yehova.—Yes. 30:18.