Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/97 tsamba 7
  • Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzira Ulosi wa Danieli!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Konzekerani Kuphunzira Ulosi wa Yesaya!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 4:
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 7/97 tsamba 7

Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja

Mudzakondwa kudziŵa kuti kuyamba ndi mlungu wa October 6, 1997, tidzaphunzira buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja pa Phunziro la Buku la Mpingo. Palibe ayenera kuphonya pophunzira monga gulu chitsogozo cha m’Malemba chimenechi cha moyo wa banja wachimwemwe. Ndandanda ya phunziro limeneli idzalola kupenda mokwana bwino ndime iliyonse ndi malemba a Baibulo amene ali m’bukumo.

Mutu wonse woyamba tidzauphunzira pamlungu woyamba wa phunzirolo, popeza ulibe kwambiri malemba osagwidwa mawu. Pachifukwa chomwechonso, mutu 15 tidzauphunzira paphunziro limodzi. Komabe, mitu ina yonse idzagaŵidwa paŵiri, nkumaphunzira ngati theka la mutu mlungu uliwonse. Choncho, padzakhala nthaŵi yokwana yoŵerenga ndi kukambitsirana malemba onse osonyezedwa limodzinso ndi kupenda mosamalitsa mmene tingagwiritsire ntchito malemba onse ogwidwa mawu m’ndime iliyonse.

Mbali yofunika ya phunziroli idzakhala kukambitsirana za m’bokosi lophunzitsa pamapeto pa mutu uliwonse. Chotero, tiyenera kugaŵa nthaŵi yokwana yokambitsirana mafunso ndi malemba osonyedwa m’bokosimo.

Otsogoza Phunziro la Buku la Mpingo akulimbikitsidwa kukonzekera phunziro lawo mosamalitsa ndi kulimbikitsa onse a m’gulu lawo, kuphatikizapo atsopano, kuti azikonzekera bwino, kupezekapo nthaŵi zonse, ndi kutengamo mbali.—om-CN 74-6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena