Kuphunzira Ulosi wa Danieli!
1 Kuyambira mlungu wa May 29, tinayamba kuphunzira buku la Samalani Ulosi wa Danieli! pa Phunziro la Buku la Mpingo. Tsopano tili ndi mwayi wopindula mwa kukambirana za m’bukuli pagulu. Ofalitsa onse, osangalatsidwa, ndiponso ana ali olandiridwa, inde, akulimbikitsidwa kupezeka mlungu uliwonse pa kuphunzira mosamalitsa buku la Baibulo la Danieli.—Deut. 31:12, 13.
2 Ndandanda Yaphunziro ndi Malangizo: Ndandanda yonse yaphunziro la buku la Ulosi wa Danieli! yalembedwa m’kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu. Onetsetsani kuti mwasunga ndandanda imeneyi m’buku lanu lophunzirira. Ndandandayi ikusonyeza mutu ndi ndime za m’buku komanso mavesi a m’Danieli omwe adzaphunziridwa pa phunziro la mlungu uliwonse. Mawu a m’munsi akufotokoza mmene mbali zina za nkhani za m’bukumo zidzapendedwere ndiponso nthaŵi yake. Pamapeto a phunziro la mlungu uliwonse, wochititsa phunziro akulimbikitsidwa kupendera limodzi ndi gulu mavesi angapo a Danieli amene alembedwa pa ndandanda ya mlungu umenewo. Ngati nthaŵi ilola, angaŵerenge ndi kugogomezera mavesiwo. Mavesi ena adzaphunziridwa kwa milungu iŵiri chifukwa chakuti matanthauzo awo akupitirizabe kupendedwa.
3 Konzekerani Phunziro Mosamalitsa: Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ali ndi udindo wapadera wokonzekera bwino. Pophunzitsa ayenera kugwiritsa ntchito bwino matchati ndi zithunzi. Zothandizira kuphunzitsa zimenezi zidzapereka mpata wabwino kwambiri woti ana achite nawo phunzirolo. Phunziro la mlungu wa September 4 liyenera kuphatikizapo kukambirana mwatsatanetsatane zithunzi ndi malemba a patsamba 139. Tchati cha patsamba 188 ndi 189 mudzakambirane pa phunziro la mlungu wa October 2.
4 Konzekerani bwino phunziro la mlungu uliwonse, ndipo sangalalani ndi kutengamo mbali. Yamikirani mwayi wanu wogwirizana ndi gulu la Yehova looneka komanso kupindula ndi chidziŵitso ndi kuzindikira zoperekedwa ndi odzozedwa ake okhulupirika. (Dan. 12:3, 4) Limbikitsani ena mokoma mtima kupezeka pa phunziro la buku nthaŵi zonse. Tonsefe tisamalire mawu aulosi a Mulungu monga mmene alembedwera m’buku lochititsa chidwi la Danieli.—Aheb. 10:23-25; 2 Pet. 1:19.