Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?
1 Pali mawu akuti ‘zimene timadya zimakhudza thanzi lathu.’ N’zoona, mphamvu ndi thanzi lathu zimadalira ndi mmene timadyera. Kudya kwathu kwauzimu nakonso kumatikhudza m’njira yabwino kapena yoipa popeza Yesu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mat. 4:4) Choncho, kodi timadya bwino mwauzimu? Kodi mumasankha zakudya? Kodi mumadya mothamanga? Kapena kodi mumasangalala kupatula nthaŵi yoti mudye zakudya zauzimu zamagulu onse, zopatsa thanzi, ndi zanthaŵi zonse?
2 Onani Zakudya Zanu: Yehova kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka “zakudya panthaŵi yake” ndi “phwando la zinthu zonona.” (Mat. 24:45; Yes. 25:6) Kuti tipindule kwambiri ndi zinthu zimenezi, tiyenera kuyesetsa kudya bwino mwauzimu.
3 Mungadzifunse kuti: ‘Kodi tsiku lililonse ndimaŵerenga lemba la tsiku ndi ndemanga yake? Kodi tsiku lililonse ndimaŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zomwe ndaŵerengazo? Kodi ndimakonzekera misonkhano yampingo mwa kuŵerenga nkhani zake? Kodi ndamaliza kuŵerenga mabuku atsopano onse, kuphatikizapo mavoliyumu onse a Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse?’
4 Yesu anati: “Achimwemwe ali ozindikira zosoŵa zawo zauzimu . . . Achimwemwe ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta.” (Mat. 5:3, 6, NW) Choncho idyani bwino mwauzimu mwa kudzadza chidziŵitso cha Mulungu m’malingaliro ndi mu mtima mwanu.