Kodi Cholinga Chathu N’chiyani?
1 N’chifukwa chiyani timachititsa maphunziro a Baibulo? Kodi timangofuna kuti anthu adziŵe Baibulo, titukule miyoyo ya anthu, kapena kuti adziŵe bwino zinthu za m’tsogolo? Ayi, si zimenezo. Cholinga chathu chenicheni ndicho kupanga ophunzira a Yesu Kristu. (Mat. 28:19; Mac. 14:21) N’chifukwa chake anthu amene timaphunzira nawo afunika kusonkhana ndi mpingo. Kukula kwawo mwauzimu kumayenderana ndi mmene akulidziŵira bwino gulu lachikristu.
2 Mmene Tingachitire Zimenezi: Mukangoyamba kuphunzira naye, musaleke kulimbikitsa wophunzirayo kupezeka pa misonkhano yampingo. (Aheb. 10:24, 25) M’fotokozereni mmene zimenezi zingalimbitsire chikhulupiriro chake, kumuthandiza kuchita zofuna za Mulungu, ndi kumuthandiza kupeza mabwenzi abwino amene akufunanso kutamanda Yehova. (Sal. 27:13; 32:8; 35:18) Kukonda ndi kuyamikira kwanu mpingo ndi misonkhano kudzam’limbikitsa kuti azipezekapo.
3 Anthu atsopano afunika kumvetsetsa kuti gulu la Yehova ndi la abale apadziko lonse. Ngati n’kotheka, aonetseni vidiyo ya Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name ndi Our Whole Association of Brothers. Athandizeni kuzindikira kuti Yehova akugwiritsa ntchito anthu odzipatulira miyandamiyanda padziko lonse kukwaniritsa zofuna zake. Auzeni atsopanowo kuti akuitanidwa kuti nawonso atumikire Mulungu.—Yes. 2:2, 3.
4 Zimasangalatsa kwambiri kuona wophunzira Baibulo akukhala wophunzira weniweni wa Yesu. Chimenechi ndiye cholinga chathu.—3 Yoh. 4.