Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/02 tsamba 3
  • Kulimbikitsana Mwapadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulimbikitsana Mwapadera
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Tipitirize Kulimbikitsana Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Misonkhano Yachigawo—Nthaŵi Yosangalala!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2006 Wakuti “Chipulumutso Chayandikira”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 7/02 tsamba 3

Kulimbikitsana Mwapadera

1 Tsiku lililonse chikhulupiriro cha anthu a Yehova chimayesedwa. Mdyerekezi, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi kochepa, akutiukira komaliza kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova. (Chiv. 12:12) Ndi bwino kuti ‘tilimbike mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake’ kuti ‘tikhoze kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, titachita zonse, tichirimike.’—Aef. 6:10, 13.

2 Kusonkhana pamodzi ndi okhulupirira anzathu ndi zimene Yehova wakonza kuti zitithandize kupeza mphamvu. Mtumwi Paulo ankadziŵa kufunika kwa zimenezi. Ankalakalaka kukhala pamodzi ndi abale ake achikristu kuti ‘atonthozedwe pamodzi’ ndi kukhala ‘okhazikika.’ (Aroma 1:11, 12) Pofuna kutilimbikitsa kuchita zimene Mulungu amafuna, Bungwe Lolamulira, chifukwa cha chikondi chake lakonza Msonkhano Wachigawo womwe ukubwerawu wakuti “Olengeza Ufumu Achangu,” kumene tikakhale ndi mwayi wopindula mwa kulimbikitsana.

3 Dzapezekenipo Kuti Mupindule: Chikhale cholinga chanu kudzapezekapo masiku onse atatu. ‘Timapindula’ mwa kufika asanaimbe nyimbo yoyamba n’kukhala nawo mpaka titanena ndi mtima wonse kuti “Amen” pa pemphero lomaliza. (Yes. 48:17, 18) Anthu ambiri akufunika kulinganiza bwino ntchito yawo msonkhanowu ukadali kutali kuti adzakhale ndi mpata wopezeka pamsonkhanowu masiku onse atatu. Ndi zoona kuti, zingakhale zovuta kupempha abwana anu kuti akupatseni tchuti, koma Yehova amatitsimikizira kuti adzatithandiza kuchita zimene iye akufuna. (1 Yoh. 5:14, 15) Ngati sitinapange zimenezi, nthaŵi yokonza za kayendedwe ndiponso malo ogona ndi ino, osangoti zidzaoneka nthaŵi yomweyo. Tikhulupirire kuti Yehova adzadalitsa zomwe tikuchita n’cholinga chakuti tikapezeke pamsonkhanowu masiku onse atatu.—Miy. 10:22.

4 Konzekerani Kukalimbikitsidwa: Kodi nthaŵi ina mutachoka kumsonkhano wachigawo, munayamba mwanenapo kuti: “Msonkhano wake unali woposa ina yonse!” Kodi n’chifukwa chiyani munanena zimenezi? Chifukwa chakuti monga anthu opanda ungwiro timatopa pang’onopang’ono, ndipo timafuna kutilimbikitsa mwauzimu. (Yes. 40:30) Mlongo wina anafotokoza kuti: “Dongosolo lino la zinthu limandifooketsa, ndipo misonkhano yachigawo imandithandiza kuikanso maganizo anga pa zinthu zauzimu, imandipatsa mphamvu zauzimu zomwe ndimafuna. Ndikuona kuti ndimalimbikitsidwa panthaŵi yeniyeni imene ndikufunitsitsa kulimbikitsidwa.” Mosakayikira munakhalapo ndi maganizo ameneŵa.

5 Timalandira chilimbikitso chimene timafuna mwa nkhani ndi kufunsa, ndiponso kudzera mu mbali zina za misonkhano yathu yachigawo zimene zimatilimbikitsa mwauzimu. Mbale wina anati: “Ndimasangalala kwambiri ndi momwe amagwiritsira ntchito bwino ndiponso momveka mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Ndiponso seŵero ndi labwino kwambiri chifukwa limasonyeza momwe tingapindulire ndi zitsanzo zakale, zabwino ndi zoipa zomwe. Mabuku atsopano ndi zinthu zimene nthaŵi zonse ndimayembekezera mwachidwi, ndipo ndimasangalala nawo kwanthaŵi yaitali ndikapita kunyumba.”

6 Misonkhano yachigawo ndi zinthu zabwino zimene Yehova watikonzera mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Tim. 3:1) Imatithandiza kulabadira malangizo ouziridwa akuti: “Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.” (1 Akor. 16:13) Choncho, tiyeni titsimikize mtima kudzapezeka pa zigawo zonse ndi kudzalimbikitsana kwambiri pa Msonkhano wathu Wachigawo wakuti “Olengeza Ufumu Achangu.”

[Bokosi patsamba 3]

Konzani Kudzapezekapo Masiku Onse Atatu

■ Pemphani tchuti kuntchito.

■ Konzani za kayendedwe popita ku msonkhano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena