Khutirani ndi Zimene Muli Nazo
1 Malemba amatilimbikitsa kuti tizipezera banja lathu zinthu zofunika m’moyo, koma zimenezi zisakhale cholinga chachikulu kwambiri m’moyo wathu. Zinthu zauzimu zizikhala patsogolo. (Mat. 6:33; 1 Tim. 5:8) Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, n’kovuta kuyendetsa mbali zonsezi popanda kunyalanyaza mbali ina. (2 Tim. 3:1) N’chiyani chingatithandize kuti tithe kusamalira mbali zonse?
2 Gwiritsani Ntchito Zimene Baibulo Limanena: Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti kufunafuna chuma kungawononge moyo wauzimu. (Mlal. 5:10; Mat. 13:22; 1 Tim. 6:9, 10) M’nthaŵi yofunika kwambiri ino, kungakhale koopsa zedi ngati wina wa ife atanganidwa kwambiri ndi ntchito kapena ndi momwe angapezere ndalama kufika pokankhira m’mbuyo zinthu zauzimu monga misonkhano, phunziro laumwini, ndi utumiki. (Luka 21:34-36) Baibulo limalangiza kuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Tim. 6:7, 8.
3 Zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu azikhala movutika mwadala. Koma zikutithandiza kuzindikira kuti zinthu zofunika pamoyo wathu ndizo chakudya, zovala ndi pogona, zimenezi zizikhala zokwanira kumene timakhala. Ngati tili ndi zinthu zofunika pamoyo, tisavutike kufuna moyo wapamwamba. Tikafuna kugula chinthu kapena kugwiranso ntchito ina, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi n’zofunika kwambiri?’ Kuchita zimenezi kudzatithandiza kumvera malangizo ouziridwa, akuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni.”—Aheb. 13:5.
4 Tikakhulupirira Yehova, iye adzatithandiza. (Miy. 3:5, 6) Ngakhale kuti timafunika kugwira ntchito molimbika kuti tipeze zofunika za tsiku lililonse, sitiika maganizo athu onse pa zinthu zimenezi. Kaya tikhale ndi zinthu zochepa kapena zambiri, timadalira Yehova kutipatsa zosoŵa zathu. (Afil. 4:11-13) Chotero timakhutira ndi zimene Mulungu amatipatsa komanso ndi madalitso ena ambiri.
5 Tsanzirani Chikhulupiriro cha Anthu Ena: Mayi wina amene alibe mwamuna amene ankalera mwana wake wamkazi m’choonadi anafeŵetsa moyo wake pang’onopang’ono. Ngakhale kuti ankasangalala kukhala m’nyumba yotakasuka imene anali kukhala, anasamukira m’nyumba yaing’ono, kenako anasamukira nyumba ya pamdadada wina. Zimenezi zinamuthandiza kuti asamagwire ntchito nthaŵi yaitali koma azikhala nthaŵi yambiri mu utumiki. Mwana wakeyo atakula ndiponso atakwatiwa, mayiyo anapuma pantchito nthaŵi yake isanakwane, ngakhale kuti zimenezi zinapangitsa kuti asamapeze ndalama zambiri. Chaka chino ndi chachisanu ndi chiŵiri, mlongo wathuyu akuchita upainiya wokhazikika ndipo sadandaula kuti anataya chuma pofuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wake.
6 Mbale wina amene ndi mkulu pamodzi ndi mkazi wake anachita upainiya kwa zaka zambiri kwinaku akulera ana awo atatu. Monga banja, anaphunzira kukhutira ndi zinthu zofunika kwambiri osati kukhutiritsa zolakalaka zawo. Mbaleyo anati: “Timakhala moyo wosafuna zambiri. Ngakhale kuti nthaŵi zina timavutika, Yehova nthaŵi zonse amatipatsa zomwe timafuna. . . . Ndikaona banja langa likutsogoza zinthu zauzimu, ndimaona kuti zonse zili bwino, ndipo ndimasangalala.” Mkazi wake anawonjezera kuti: “Ndikaona [mwamuna wanga] atatanganidwa ndi zinthu zauzimu, ndimasangalala kwambiri mu mtima.” Ananso amasangalala kuti makolo awo anasankha kutumikira Yehova nthaŵi zonse.
7 Onse amene asankha kudzipereka kuchita ntchito ya Mulungu osati kufunafuna chuma, Baibulo limawalonjeza kuti adzapeza madalitso ambiri panopo ndiponso moyo ukubwerawo.—1 Tim. 4:8.