Kodi Tiyenera Kukumbukira Chiyani Pogwiritsa Ntchito Mafoni a M’manja ndi Mapeja?
1 Zinthu zimenezi zingatithandize kulankhulana ndi anthu ena pafupifupi kulikonse kumene tili. Ngakhale kuti zinthuzi n’zothandiza, tifunika kusamala. Tisalole kuti mafoni a m’manja ndiponso mapeja azidodometsa utumiki wathu kapena misonkhano yathu yachikristu. Kodi zingadodometse bwanji?
2 Taganizirani zimene zingachitike ngati foni yathu ya m’manja kapena peja yalira tili mkati molalikira. Kodi mwininyumba angaganize chiyani? Kodi angaganize chiyani ngati tisiya kaye kulankhula naye kuti tiyankhe foni kapena peja? Sitingafune kuchita chilichonse chimene chingalepheretse anthu ena kumvera uthenga wa Ufumu. (2 Akor. 6:3) Choncho, ngati tatenga foni kapena peja, tiitchere moti isatidodometse kapena kudodometsa ena pamene tili muutumiki wakumunda.
3 Bwanji ngati ife tikudikira pamene anzathu akulalikira? Ngati tapatula nthawi yochita utumiki wakumunda, kodi si bwino kuika maganizo athu pa ntchito imeneyi? Pofuna kulemekeza utumiki wathu wopatulika, ndi bwino kukambirana nkhani zina kapena kucheza panthawi ina. (Aroma 12:7) Koma izi sizikutanthauza kuti sitingagwiritse ntchito foni popitiriza ulaliki kapena kupangana ndi munthu nthawi yodzacheza naye.
4 Tiyenera kusamala kwambiri pankhani ya kugwiritsa ntchito mafoni a m’manja pamene tikuyendetsa galimoto, chifukwa kafukufuku akusonyeza kuti zimenezi zimachititsa ngozi. Tiyenera kutsatira malamulo onse oletsa kugwiritsa ntchito mafoni a m’manja poyendetsa galimoto.
5 Timapita ku misonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo kukalambira Yehova ndiponso kuti akatiphunzitse. Kodi kuzindikira kupatulika kwa misonkhano imeneyi sikuyenera kutilimbikitsa kutchera mafoni a m’manja ndi mapeja moti asatidodometse ndiponso kudodometsa anthu ena? Ngati pali nkhani imene tikufunika kuti tiisamalire mwachangu, tiyenera kutuluka ndi kukayankha foni panja, osati pamisonkhano. Apo ayi, tizikonza zokambirana nkhani zathu kapena nkhani wamba panthawi ina osati nthawi yolambira.—1 Akor. 10:24.
6 Mmene timagwiritsira ntchito foni ya m’manja kapena chipangizo chilichonse ziyenera kusonyeza kuti timaganizira ena ndiponso timayamikira kwambiri zinthu zauzimu.