Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingatithandize kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito mafoni a m’manja tikakhala pa misonkhano yachikhristu komanso mu utumiki?
“Chilichonse Chili ndi Nthawi Yake.” (Mlal. 3:1): Mafoni amathandiza anthu kuti azilankhulana komanso kutumizirana mameseji pa nthawi ina iliyonse. Komabe, pa zochitika zina Akhristu safuna kuti azisokonezedwa ndi mafoni awo. Mwachitsanzo, misonkhano yathu imakhala nthawi yolambira Yehova, kulangizidwa mwauzimu komanso kulimbikitsana. (Deut. 31:12; Sal. 22:22; Aroma 1:11, 12) Choncho tiyenera kuzimitsa mafoni athu tikangofika pa misonkhano ndipo sitiyenera kumawerenga mameseji pa foni yathu mpaka misonkhano itatha. Ngati pali chifukwa chomveka chosazimitsira foni yathu, tiyenera kuitchera kuti isasokoneze anthu ena.
‘Chitani Zinthu Zonse Chifukwa cha Uthenga Wabwino.’ (1 Akor. 9:23): Nthawi zina, pamakhala zifukwa zomveka zogwiritsira ntchito foni mu utumiki. Mwachitsanzo, m’bale amene akutsogolera mu utumiki angagwiritsire ntchito foni poimbira ofalitsa ena amene akulalikira m’dera lina. Ofalitsa ena nthawi zina amagwiritsira ntchito mafoni awo kuimbira munthu wina wachidwi kapena wophunzira Baibulo asanakaphunzire naye, makamaka ngati munthuyo amakhala kutali. Ngati tili ndi foni, tiyenera kukhala osamala kuti isatisokoneze pamene tikulankhula ndi munthu mu utumiki. (2 Akor. 6:3) Poyembekezera anzathu mu utumiki, tiyenera kuika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira ndiponso kuthandiza anzathu amene tikulalikira nawo limodzi m’malo motanganidwa ndi kuimba mafoni kapena kutumizirana mameseji.
Tiziganizira Ena. (1 Akor. 10:24; Afil. 2:4): Tisakhale ndi chizolowezi chochedwa kufika pa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda pokhala ndi maganizo akuti tiimbira foni wofalitsa wina kapena kumutumizira meseji kuti tidziwe kumene akulalikira. Tikafika mochedwa zimapangitsa kuti kaguluko kagawidwenso. N’zoona kuti pangakhale zifukwa zomveka zimene zingachititse kuti nthawi zina tichedwe mu utumiki. Komabe, tikakhala ndi chizolowezi chofika mofulumira, timasonyeza kuti timalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa komanso kuti timaganizira m’bale amene akutsogolera mu utumiki ndiponso ofalitsa anzathu.