Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/02 tsamba 8
  • Khalani Ogwirizana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Ogwirizana
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Mgwirizano wa Akhristu Umalemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Umodzi Weniweni Wachikristu—Kodi Umatheka Motani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Tingathandize Bwanji Kulimbitsa Mgwirizano Wathu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 7/02 tsamba 8

Khalani Ogwirizana

1 Kodi n’kangati mwakhala mukuchita chidwi ndi mmene anapangira mwaluso thupi la munthu? (Sal. 139:14) Chiwalo chilichonse chimagwira ntchito mogwirizana ndi ziwalo zina. Mawu a Mulungu amayerekezera mpingo wachikristu ndi thupi logwira ntchito bwino. Motsogoleredwa ndi Mutu, yemwe ndi Kristu, anthu onse a mumpingo ndi ‘okowanidwa ndi olumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse.’ (Aef. 4:16a) Chotero, Yehova amagwiritsa ntchito anthu ake ogwirizana kuchita zinthu zodabwitsa kwambiri.

2 Anthu a mu mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, anasamalirana pa zosoŵa zauzimu ndiponso zakuthupi “ndi mtima umodzi.” (Mac. 2:44-47) Chifukwa chakuti Yehova anawathandiza, mogwirizana, analimbana ndi chitsutso chankhanza ndipo anachigonjetsa. (Mac. 4:24-31) Kulikonse kumene anapita analalikira uthenga wa Ufumu, anafalitsa uthenga wabwino mbali yonse ya dziko imene inali yodziŵika panthaŵiyo. (Akol. 1:23) Masiku ano, mpingo wachikristu wachita mogwirizana zinthu zofananazi ku mlingo waukulu. Kodi n’chiyani chimene chimawapangitsa kuti azigwirizana choncho?

3 Chiphunzitso cha Mulungu Chimawagwirizanitsa: Ndife ogwirizana padziko lonse lapansi chifukwa cha kulambira kwathu. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Timazindikira njira yooneka ndi maso imene Yehova amaperekera “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mat. 24:45) Timayamikiranso kwambiri “mphatso mwa amuna” zimene wapereka kukhala aphunzitsi mu mpingo. Tikavomereza modzichepetsa njira imene Yehova amatidyetsera mwauzimu, kudziŵa kwathu Mawu a Mulungu kumakula ndipo kumatilimbikitsa kukhala ndi chikhumbo chimene ambiri ali nacho chofuna kutsanzira Yesu monga ophunzira ake. Tiyenera kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu, kuyesetsa ndi mtima wonse kuti ‘tifikire ku umodzi wa chikhulupiriro.’ (Aef. 4:8, 11-13) Kodi mukulimbikitsa mgwirizano wathu wauzimu mwa kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse?

4 Ogwirizana Chifukwa Choyanjana ndi Akristu: Chikondi chimatigwirizanitsa pamodzi pamisonkhano yachikristu. Pamisonkhano imeneyi, ‘timaganizirana wina ndi mnzake.’ (Aheb. 10:24, 25) Izi zimatanthauza osati kuona maonekedwe amunthu okha ayi, koma kuwadziŵadi abale athu, kuwaona kukhala ofunika monga momwe Yehova amawaonera. (Hag. 2:7) Pamene atiuza za chikhulupiriro chawo, timawakonda kwambiri ndipo mgwirizano wathu umalimba. Kodi mumadziŵika kuti mumafika pamisonkhano yampingo nthaŵi zonse?

5 Antchito Anzathu M’munda: Kulalikira uthenga wabwino ndi okhulupirira anzathu kumatithandiza kukhala ogwirizana pochita chifuno cha Mulungu. Mtumwi Paulo anakonda ‘antchito anzake a mu Ufumu wa Mulungu.’ (Akol. 4:11) Kukambirana zokumana nazo ndiponso kuthandizana mu utumiki kumatithandiza kukwaniritsa ntchito yathu yachikristu ndiponso kumalimbitsa mgwirizano wathu.—Akol. 3:14.

6 Mphamvu ya Mzimu Woyera Imatigwirizanitsa: Tikalimbikira kuchita chifuno cha Yehova, iye amatipatsa mzimu wake. Zimenezi zimatithandiza kuthetsa mikangano ndiponso kuti tizikhala mogwirizana ndi anzathu. (Sal. 133:1) Umatilimbikitsa “kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.” (Aef. 4:3) Aliyense wa ife angalimbikitse mgwirizano umene uli pakati pa anthu a Mulungu mwa kusonyeza chipatso cha mzimu pa zimene timachitira ena.—Agal. 5:22, 23.

7 Kutumikira pamodzi motsogoleredwa ndi Kristu ‘kumachita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.’ (Aef. 4:16b) Komanso, kumalemekeza Yehova, “Mulungu wa mtendere.”—Aroma 16:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena