Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 November tsamba 28-29
  • “Muziyesetsa ndi Mtima Wonse Kusunga Umodzi Umene Timaupeza Mothandizidwa ndi Mzimu Woyera”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Muziyesetsa ndi Mtima Wonse Kusunga Umodzi Umene Timaupeza Mothandizidwa ndi Mzimu Woyera”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘MUZIYESETSA NDI MTIMA WONSE’ KUKHALA MOGWIRIZANA
  • Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mgwirizano wa Akhristu Umalemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Sungani Umodzi m’Masiku Ano Otsiriza
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kusungirira Umodzi Wathu Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 November tsamba 28-29
Abale ndi alongo akudya chakudya limodzi mosangalala kunyumba ya m’bale wina.

“Muziyesetsa ndi Mtima Wonse Kusunga Umodzi Umene Timaupeza Mothandizidwa ndi Mzimu Woyera”

MTUMWI Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti ‘azilolerana chifukwa cha chikondi. Aziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera, pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.’—Aef. 4:​2, 3.

“Umodzi,” kapena kuti mgwirizano umene timasangalala nawo “timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.” Zimenezi zikusonyeza kuti ndi Mulungu amene amatithandiza. Komabe, mogwirizana ndi zimene Paulo ananena, pamafunika khama kuti tipitirize kukhala ogwirizana. Kodi ndi ndani ayenera kuchita zimenezi? Mkhristu aliyense ayenera kuyesetsa “kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.”

Tiyerekeze kuti munthu wina wakupatsani galimoto yanyuwani. Kodi ndi ndani amene ali ndi udindo woisamalira? Yankho lake ndi lodziwikiratu. Simungaimbe mlandu munthu amene anakupatsani galimotoyo ngati itawonongeka chifukwa choti simukuisamalira.

Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti umodzi wathu ndi mphatso imene Mulungu anatipatsa, aliyense wa ife ali ndi udindo wolimbikitsa mgwirizanowu. Ngati sitikugwirizana ndi Mkhristu mnzathu, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuchita mbali yanga kuti tipitirize kukhala mogwirizana poyesetsa kuthetsa nkhaniyo?’

‘MUZIYESETSA NDI MTIMA WONSE’ KUKHALA MOGWIRIZANA

Mogwirizana ndi zimene Paulo ananena, nthawi zina tingafunike kuchita khama kuti tizikhala mogwirizana, makamaka pamene m’bale kapena mlongo wathu watikhumudwitsa. Kuti tipitirize kukhala mwamtendere, kodi nthawi zonse timafunika kupita kukakambirana ndi munthu amene tasemphana naye maganizo? Osati kwenikweni. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi kukambirana nkhaniyi kulimbikitsa mgwirizano kapena kungowonjezera mavuto?’ Nthawi zina zingakhale bwino kungonyalanyaza nkhaniyo kapena kukhululuka.—Miy. 19:11; Maliko 11:25.

Zithunzi: M’bale akusankha kunyalanyaza zimene walakwiridwa. 1. Ndiyeno m’bale wina akumukalipira. 2. Iye akuganizira zimene m’bale uja wachita. 3. Kenako akuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama.

Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi kukambirana nkhaniyi kulimbikitsa mgwirizano kapena kungowonjezera mavuto?’

Mogwirizana ndi zimene Paulo analemba, nthawi zonse ‘tizilolerana chifukwa cha chikondi.’ (Aef. 4:2) Buku lina linamasulira mawuwa kuti “muziwalandira mmene alili.” Kutanthauza kuti tizivomereza kuti abale ndi alongo athu ndi ochimwa ngati mmene ifeyo tilili. N’zoona kuti timayesetsa kuvala “umunthu watsopano.” (Aef. 4:​23, 24) Komabe palibe amene angachite zimenezi mosalakwitsa. (Aroma 3:23) Kudziwa mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tisamavutike kuleza mtima n’kumakhululukirana komanso ‘kumasunga umodzi wathu mwamzimu.’

Tikamakhululukira abale ndi alongo athu, tidzapitiriza kukhala “mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.” Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chomangira chimene chimatigwirizanitsa” pa Aefeso 4:3 anawamasulira kuti “minyewa” pa Akolose 2:19. Minyewa ndi yamphamvu kwambiri ndipo imalumikizitsa mafupa. Mofanana ndi zimenezi, mtendere komanso kukonda abale athu zimathandiza kuti tizigwirizana nawo kwambiri ngakhale kuti timasemphana zinthu zina.

Choncho ngati Mkhristu mnzanu wakulakwirani, kukukhumudwitsani kapena kukukwiyitsani muzimuchitira chifundo m’malo momuweruza. (Akol. 3:12) Tonsefe si angwiro, choncho nthawi zina timakhumudwitsa anthu ena. Kukumbukira mfundo imeneyi kungakuthandizeni kuti muzichita mbali yanu ‘poyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena