Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 November tsamba 22-27
  • “Ndiwe Munthu Wokondedwa Kwambiri”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndiwe Munthu Wokondedwa Kwambiri”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MMENE YESU ANATHANDIZIRA ANTHU KUTI AZIDZIONA KUTI NDI AMTENGO WAPATALI
  • ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZIDZIONA MMENE YEHOVA AMAKUONERANI
  • “Ambuye Ndawaona Ine!”
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Yehova “Amachiritsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Yehova Amakukondani Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Zimene Tikuphunzira kwa Yesu pa Masiku Ake 40 Omaliza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 November tsamba 22-27

NKHANI YOPHUNZIRA 47

NYIMBO NA. 38 Adzakulimbitsa

“Ndiwe Munthu Wokondedwa Kwambiri”

“Ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.”—DAN. 9:23.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi ithandiza anthu amene amadziona kuti ndi osafunika kudziwa kuti Yehova amawakonda kwambiri.

1-2. Kodi tingatani kuti tisamakayikire zoti ndife amtengo wapatali kwa Yehova?

PAKATI pa atumiki a Yehova amtengo wapatali, pali ena amene amadziona kuti ndi osafunika. N’kutheka kuti wina anawachitira zinthu ngati kuti ndi opanda ntchito. Kodi inunso zimenezi zinakuchitikiranipo? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muzidziona kuti ndinu wamtengo wapatali kwa Yehova?

2 Mungachite bwino kuwerenga nkhani za m’Baibulo zosonyeza zimene Yehova amafuna kuti anthu azichitira anzawo komanso mmene ayenera kuwaonera. Mwana wake Yesu, ankalemekeza anthu ndipo ankawachitira zinthu mwachifundo. Pochita zimenezi, anasonyeza kuti iyeyo komanso Atate wake amaona kuti anthu amene amadziona kuti ndi osafunika ndi amtengo wapatali kwambiri. (Yoh. 5:19; Aheb. 1:3) Munkhaniyi tikambirana: (1) mmene Yesu anathandizira anthu kuona kuti ndi ofunika komanso (2) zimene tingachite kuti tisamakayikire zoti Mulungu amationa kuti ndife amtengo wapatali.—Hag. 2:7.

MMENE YESU ANATHANDIZIRA ANTHU KUTI AZIDZIONA KUTI NDI AMTENGO WAPATALI

3. Kodi Yesu anachita bwanji zinthu ndi anthu a ku Galileya amene ankafuna kuti awathandize?

3 Pa nthawi imene Yesu ankalalikira pa ulendo wachitatu ku Galileya, anthu ambiri am’madera osiyanasiyana ankapita kwa iye kuti akamvetsere zimene ankaphunzitsa komanso akawachiritse. Yesu anaona kuti anali “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mat. 9:36) Atsogoleri awo achipembedzo ankawaona kuti ndi osafunika ndipo ankawatchula kuti ndi anthu ‘otembereredwa.’ (Yoh. 7:​47-49) Koma Yesu anasonyeza kuti ankawalemekeza powaphunzitsa komanso kuwachiritsa matenda awo. (Mat. 9:35) Pofuna kuthandiza anthu ambiri, Yesu anaphunzitsa atumwi ake kuti azitha kugwira ntchito yolalikira ndipo anawapatsa mphamvu kuti azichiritsa odwala.—Mat. 10:​5-8.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu omwe ankamumvetsera?

4 Pochita zinthu mwaulemu komanso mwachifundo ndi anthu amene ankamumvetsera, Yesu anasonyeza kuti iyeyo komanso Atate wake, amaona kuti anthu amene ena amawaona kuti ndi osafunika, ndi amtengo wapatali. Ngati mumatumikira Yehova koma mumadziona ngati ndinu osafunika, muziganizira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu amene ankafuna kuti awaphunzitse. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mudziwe kuti ndinu amtengo wapatali kwa Yehova.

5. Fotokozani mmene zinthu zinalili pa moyo wa mayi amene Yesu anakumana naye ku Galileya?

5 Sikuti Yesu ankangophunzitsa anthu monga gulu, koma ankachitanso chidwi ndi munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, Yesu akuchita utumiki wake ku Galileya, anakumana ndi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. (Maliko 5:25) Popeza matenda ake ankamupangitsa kuti akhale wodetsedwa, aliyense womukhudza akanakhalanso wodetsedwa. Zimenezi ziyenera kuti zinkapangitsa kuti asamachite zinthu ndi ena. Kuwonjezera pamenepo, sankatha kulambira Yehova limodzi ndi anthu ena kusunagoge komanso pa nthawi ya zikondwerero. (Lev. 15:​19, 25) N’zosakayikitsa kuti mayiyu, sikuti ankangovutika ndi matenda okhawa komanso ankadziona kuti ndi wachabechabe.—Maliko 5:26.

6. Kodi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi anachiritsidwa bwanji?

6 Mayi amene ankadwala matenda aakuluyu, ankafuna kuti Yesu amuchiritse. Koma sanapite mwachindunji kukamupempha kuti amuchiritse. Chifukwa chiyani? Mwina ankachita manyazi chifukwa cha matenda akewa. N’kuthekanso kuti ankachita mantha kuti Yesu amukalipira, chifukwa anapita pagulu la anthu akudziwa kuti ndi wodetsedwa. Choncho iye anangogwira malaya akunja a Yesu ndipo ankakhulupirira kuti akangochita zimenezi, basi achira. (Maliko 5:​27, 28) Chikhulupiriro chake chinamuthandiza chifukwa anachiritsidwa. Kenako Yesu anafunsa kuti adziwe amene anamugwira ndipo mayiyo anavomera kuti ndi iyeyo. Ndiye kodi Yesu anamutani?

7. Kodi Yesu anachita bwanji zinthu ndi mayi amene ankadwala matenda aakulu? (Maliko 5:34)

7 Yesu anachita zinthu ndi mayiyo mwaulemu komanso mokoma mtima. Iye anazindikira kuti ‘ankachita mantha komanso kunjenjemera.’ (Maliko 5:33) Atazindikira mmene ankamvera, Yesu anamulankhula mokoma mtima komanso anamulimbikitsa. Ndipo Yesu anamutchula kuti “Mwanawe,” mawu amene amasonyeza ulemu komanso kukoma mtima ndi chikondi. (Werengani Maliko 5:34.) Iyi ndi nthawi imodzi yokha imene Yesu anatchula mwachindunji mayi kuti “mwanawe” mwina chifukwa anaona kuti mayiyo ankachita mantha komanso ‘kunjenjemera.’ Mayiyu ayenera kuti mtima wake unakhala m’malo. Yesu akanakhala kuti sanamulankhule mwachifundo, n’zoona kuti mayiyu akanachira, koma akanapita kwawo ali ndi nkhawa komanso akudziimba mlandu. M’malomwake, Yesu anamuthandiza kuti azidziona mmene analilidi, kuti ndi mwana wamtengo wapatali wa Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi.

8. Kodi mlongo wa ku Brazil ankakumana ndi mavuto otani?

8 Masiku anonso, atumiki ena a Mulungu amavutika ndi matenda amene amawapangitsa kuti azidzimva kuti ndi achabechabe. Mlongo wina wa ku Brazil yemwe ndi mpainiya dzina lake Maria,a anabadwa wolumala ndipo alibe miyendo komanso mkono wakumanzere. Iye anati: “Nthawi zambiri kusukulu anzanga ankandiseka chifukwa choti ndine wolumala. Komanso ankandipatsa mayina ambiri achipongwe. Ngakhale anthu am’banja langa ankandisala.”

9. N’chiyani chinathandiza Maria kuti azidziona kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

9 Kodi Maria anathandizidwa bwanji? Atakhala wa Mboni za Yehova, Akhristu anzake anamulimbikitsa komanso kumuthandiza kuti azidziona mmene Yehova amamuonera. Iye anati: “Buku langa linadzadza moti mulibe malo okwanira oti ndilembe dzina la aliyense amene anandithandiza. Ndimathokoza Yehova ndi mtima wonse pondipatsa banja labwino lauzimu.” Abale ndi alongo auzimu a Maria, anamuthandiza kuzindikira kuti ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu.

10. Kodi ndi mavuto ati amene Mariya wa ku Magadala ankakumana nawo? (Onaninso zithunzi.)

10 Taganiziraninso mmene Yesu anathandizira Mariya wa ku Magadala. Iye anali atagwidwa ndi ziwanda 7. (Luka 8:2) Chifukwa chakuti anagwidwa ndi ziwanda, n’kutheka kuti ankachita zinthu zachilendo zimene zinkapangitsa kuti ena azimupewa. Pa nthawi imeneyo, n’kutheka kuti ankaona kuti anthu amamusala, sangamukonde komanso kumuthandiza. N’zosakayikitsa kuti Yesu anachotsa ziwanda zomwe zinkamuzunzazo, ndipo anakhala wophunzira wake wodzipereka. Kodi ndi njira zinanso ziti zimene Yesu anathandizira Mariya wa ku Magadala kumvetsa kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

Zithunzi: 1. Yesu akuchita chidwi ndi Mariya wa ku Magadala yemwe wagwada pakanjira kakang’ono. 2. Mariya wa ku Magadala akusangalala kuyenda limodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.

Kodi Yesu anatsimikizira bwanji Mariya wa ku Magadala kuti anali wofunika kwa Yehova? (Onani ndime 10 ndi11)


11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Mariya wa ku Magadala anali wamtengo wapatali kwa Mulungu? (Onaninso zithunzi.)

11 Yesu anapempha Mariya wa ku Magadala kuti aziyenda naye limodzi akamalalikira.b Zimenezi zinathandiza kuti Mariya azipindula akamamva Yesu akuphunzitsa ena. Yesu anaonekeranso kwa iye pa tsiku limene anaukitsidwa. Mariya anali mmodzi mwa ophunzira oyambirira amene Yesu analankhula nawo pa tsikuli. Ndipotu Yesu anamutuma kuti akauze atumwi ake zoti iye waukitsidwa. Zimenezi zinali umboni wakuti Mariya ndi wamtengo wapatali kwa Yehova.—Yoh. 20:​11-18.

12. Fotokozani zimene zinkachititsa Lidia kudzimva kuti ndi wachabechabe.

12 Anthu ambiri masiku ano, amavutika ndi maganizo odziona kuti ndi achabechabe ngati mmene zinalili ndi Mariya wa ku Magadala. Mlongo wina wa ku Spain dzina lake Lidia, ananena kuti mayi ake ali ndi mimba ya iyeyo, ankaganiza zoichotsa. Iye amakumbukira kuti ngakhale ali mwana, mayi ake sankamusamalira ndipo ankamunyoza. Iye anati: “Ndinkafunitsitsa anthu ena atamandisonyeza chikondi. Ndinkaganiza kuti palibe angamandikonde chifukwa mayi anga ankandipangitsa kudzimva kuti ndine munthu woipa.”

13. N’chiyani chinathandiza Lidia kuyamba kudziona kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

13 Lidia atayamba kuphunzira Baibulo, zinthu zinasintha pa moyo wake. Kupemphera, kuwerenga Baibulo, zolankhula komanso zochita za abale ndi alongo, zinamuthandiza kudziwa kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. Iye anati: “Nthawi zambiri mwamuna wanga amandiuza kuti amandikonda kwambiri ndipo amandiuza za makhalidwe anga abwino. Anzanga enanso apamtima amachita zomwezo.” Kodi pali winawake amene akufunika kuthandizidwa kumvetsa kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZIDZIONA MMENE YEHOVA AMAKUONERANI

14. Kodi lemba la 1 Samueli 16:​7, limatithandiza bwanji kudziwa mmene Yehova amaonera anthu? (Onani bokosi lakuti “N’chifukwa Chiyani Yehova Amaona Kuti Anthu Ake Ndi Amtengo Wapatali?”)

14 Muzikumbukira kuti Yehova amakuonani mosiyana ndi mmene anthu am’dzikoli amakuonerani. (Werengani 1 Samueli 16:7.) Iye samakuonani kuti ndinu ofunika potengera mmene mumaonekera, ndalama zimene muli nazo kapenanso maphunziro anu. (Yes. 55:​8, 9) Choncho m’malo modziona ngati mmene anthu am’dzikoli amakuonerani, muzidziona kuti ndinu wofunika ngati mmene Yehova amakuonerani. Mungawerenge nkhani za m’Baibulo zosonyeza mmene Yehova ankakondera anthu, omwe pa nthawi inayake ankadzikayikira monga Eliya, Naomi ndi Hana. Mungalembenso zomwe zinakuchitikirani, zimene zimakutsimikizirani kuti Yehova amakukondani komanso amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Kuwonjezera pamenepa, mukhozanso kuwerenga nkhani za m’mabuku athu zomwe zingakuthandizeni kuti muzidziona kuti ndinu wofunika.c

N’chifukwa Chiyani Yehova Amaona Kuti Anthu Ake Ndi Amtengo Wapatali?

Yehova analenga anthu m’njira yosiyana kwambiri ndi zinyama. Iye anatilenga m’njira yakuti tikhoza kumudziwa bwino n’kukhala anzake. (Gen. 1:27; Sal. 8:5; 25:14; Yes. 41:8) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamadzione kuti ndife achabechabe. Komabe tikakhala anzake, tikamamumvera komanso kudzipereka kwa iye, m’pamene timakhala amtengo wapatali kwa Mulungu, yemwenso ndi Mlengi wathu.—Yes. 49:15.

15. N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti Danieli ndi “wokondedwa kwambiri”? (Danieli 9:23)

15 Muzikumbukira kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wofunika chifukwa cha kukhulupirika kwanu. Pa nthawi ina mneneri Danieli, mwina ali ndi zaka za m’ma 90, ankadzimva kuti ndi ‘wotopa kwambiri’ komanso anali wokhumudwa. (Dan. 9:​20, 21) Ndiye kodi Yehova anamulimbikitsa bwanji? Iye anatumiza mngelo Gabirieli kuti akauze Danieli kuti ndi “wokondedwa kwambiri” komanso kuti Mulungu wamva mapemphero ake. (Werengani Danieli 9:23.) N’chiyani chinkapangitsa Danieli kuti akhale wamtengo wapatali kwa Mulungu? Kuwonjezera pa makhalidwe ake abwino, Danieli ankakonda chilungamo komanso anali wokhulupirika. (Ezek. 14:14) Yehova analola kuti nkhani imeneyi ilembedwe m’Mawu ake kuti izitilimbikitsa. (Aroma 15:4) Yehova amamvetseranso mapemphero anu ndipo amakuonani kuti ndinu amtengo wapatali chifukwa mumakonda chilungamo komanso mumamutumikira mokhulupirika.—Mika 6:​8, mawu am’munsi; Aheb. 6:10.

16. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona kuti Yehova ndi bambo wachikondi?

16 Muziona kuti Yehova ndi bambo amene amakukondani. Iye amafuna kukuthandizani osati kukupezerani zifukwa. (Sal. 130:3; Mat. 7:11; Luka 12:​6, 7) Kuganizira mfundoyi kwathandiza anthu ambiri amene amadziona kuti ndi achabechabe. Mwachitsanzo, taganizirani za mlongo wina wa ku Spain dzina lake Michelle, yemwe ankadzimva kuti ndi wachabechabe komanso wosafunika chifukwa choti kwa zaka zambiri, mwamuna wake ankamulankhula zachipongwe. Iye anati: “Ndikamadzimva kuti ndine wachabechabe, ndimayerekezera Yehova atandinyamula m’manja mwake, akundisonyeza chikondi komanso kunditeteza.” (Sal. 28:9) Mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Lauren ananena kuti: “Ngati Yehova mokoma mtima anandikokera kwa iye ndi zingwe zachikondi ndipo wakhala akundikonda kwa zaka zonsezi moti anandigwiritsapo ntchito pophunzitsa ena, sindikayikira kuti amandiona kuti ndine wofunika komanso wamtengo wapatali.”—Hos. 11:4.

17. N’chiyani chingakutsimikizireni kuti Yehova akusangalala nanu? (Salimo 5:12) (Onaninso chithunzi.)

17 Musamakayikire kuti Yehova amasangalala nanu. (Werengani Salimo 5:12.) Davide anayerekezera mfundo yakuti Yehova amasangalala nafe ndi “chishango chachikulu” choteteteza anthu olungama. Kudziwa kuti Yehova amasangalala nafe komanso amatithandiza, kungatiteteze tikayamba kudzikayikira. Kodi mungadziwe bwanji kuti Yehova amasangalala nanu? Monga taonera, Yehova amakutsimikizirani kudzera m’Mawu ake. Iye amagwiritsanso ntchito akulu, anzanu apamtima komanso anthu ena pofuna kukutsimikizirani kuti ndinu amtengo wapatali kwa iye. Kodi muzitani ena akakulimbikitsani mwa njira imeneyi?

Mlongo akumwetulira pamene akuchoka pa Nyumba ya Ufumu kuti akalowe nawo mu utumiki, ndipo mlongo wina wamugwira paphewa.

Kudziwa kuti Yehova amasangalala nafe kungatithandize kuti tisamadzione kuti ndife osafunika (Onani ndime 17)


18. N’chifukwa chiyani mumafunika kuvomereza wina akakuyamikirani?

18 Anthu amene amakukondani komanso kukudziwani akakuyamikirani, musamaone ngati akukokomeza. Muzikumbukira kuti Yehova akhoza kukhala kuti akuwagwiritsa ntchito, kuti akuthandizeni kudziwa kuti iyeyo akusangalala nanu. Michelle yemwe tamutchula uja anati: “Pang’ono ndi pang’ono ndikuphunzira kuti ndisamakayikire ena akandiyamikira. Ngakhale kuti n’zovuta, ndikudziwa kuti n’zimene Yehova akufuna kuti ndizichita.” Akulu anamuthandizanso mokoma mtima kudziwa kuti Yehova amamukonda. Panopa Michelle akuchita upainiya ndipo amathandizira ntchito zina za ku Beteli ali kunyumba.

19. N’chiyani chimakutsimikizirani kuti ndinu wofunika kwa Mulungu?

19 Yesu amatikumbutsa kuti ndife ofunika kwambiri kwa Atate wathu wakumwamba. (Luka 12:24) Choncho sitingakayikire kuti Yehova amationa kuti ndife amtengo wapatali. Tisamaiwale mfundo imeneyi. Ndipo tiziyesetsa kuthandiza ena kuona kuti ndi amtengo wapatali kwa Yehova.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kuzindikira kuti ndi amtengo wapatali kwa Mulungu?

  • Kodi Yesu anathandiza bwanji mayi amene ankadwala matenda otaya magazi?

  • N’chiyani chingatithandize kuti tizidziona mmene Yehova amationera?

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

a Mayina ena asinthidwa.

b Zikuoneka kuti Mariya wa ku Magadala anali mmodzi wa amayi amene ankayenda ndi Yesu. Amayiwa ankathandiza Yesu ndi atumwi ake pogwiritsa ntchito chuma chawo.—Mat. 27:​55, 56; Luka 8:1-3.

c Mwachitsanzo, onani mutu 24 m’buku la Yandikirani Yehova ndipo werengani malemba ndi nkhani za m’Baibulo pansi pa mutu wakuti “Kudzikayikira,” m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena