Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 15
“Kodi mukuganiza kuti tiyenera kukhala okhulupirika kwambiri kwa ndani? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikugogomezera kuti tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu woona. [Pitani patsamba 5, ndipo ŵerengani 2 Samueli 22:26, NW.] Kodi mumadziŵa kuti kukhulupirika kwa Mulungu kungathandize anthu kusachitira anzawo zoipa? Ndikukhulupirira kuti mukasangalala kuŵerenga za nkhani imeneyi.”
Galamukani! Aug. 8
“Anthu ambiri amaona kutchova njuga ngati maseŵera abwino otayirapo nthaŵi. Ena amaona kuti nthaŵi zambiri kumawonongetsa mabanja ndiponso anthu m’deralo sakhalitsana bwino. Galamukani! iyi ikupenda nkhani ya kutchova njuga malinga ndi zimene kafukufuku wina posachedwapa wasonyeza pankhaniyi. Mukhoza kusangalalanso kuŵerenga zimene mfundo za m’Baibulo zimanena pankhaniyi.” Pomusonyeza chitsanzo, ŵerengani 1 Timoteo 6:10.
Nsanja ya Olonda Sep. 1
“Kodi mwaona kuti m’madera ambiri anthu oyandikana nyumba sadziŵana monga ankachitira kale? [Yembekezani ayankhe.] Yesu anatchula mfundo ya makhalidwe abwino yomwe ndi yofunika kwambiri kuti tikhale mnansi wabwino. [Ŵerengani Mateyu 7:12.] Nkhani izi zikusonyeza momwe tingakhalire anansi abwino ndiponso momwe tingalimbikitsire ena kuchita zomwezo.”
Galamukani! Sep. 8
“Anthu ambiri akuda nkhaŵa kwambiri ndi kuchuluka kwa ziwawa ndi uchigaŵenga. Mwina mukuvomereza mawu a Mlaliki 8:9. [Ŵerengani lembali ndipo yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikufotokoza zimene tingaphunzire pa zinthu zakale ndiponso momwe kupwetekana kumeneku kuthere posachedwapa.”