Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct.15
“Kodi mungawafotokozere bwanji ana kapena anthu ena chifukwa chake masiku ano pamachitika zinthu zambiri zoipa? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limayankha funso lakuti, ‘Kodi Ndani Amene Amachititsa Kuipa Konseku?’ [Ŵerengani 1 Yohane 5:19.] Magazini ya Nsanja ya Olonda iyi ikuthandizani kudziŵa woipa ameneyu ndiponso momwe tingam’kanire.”
Galamukani! Oct. 8
“Anthu ambiri masiku ano akuda nkhaŵa kwambiri ndi zigaŵenga, komanso zida zofalitsa tizilombo topereka matenda. Kodi mukuganiza kuti maboma a anthu angathetse uchigaŵenga padziko lapansi pano? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena zimene Mulungu akufuna kuchita. [Ŵerengani Ezekieli 34:28.] Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zina zokhudza nkhaniyi.”
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Ambirife timayesetsa kukhala bwino ndi anthu ena. Koma simungakane kuti zimenezi n’zovuta nthaŵi zambiri, si choncho? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limafotokoza chifukwa chake zinthu zili chonchi. [Ŵerengani Yakobo 3:2.] Nkhani iyi ikusonyeza mmene kupepesa kungathandizire kukhazikitsa ndi kusungitsa mtendere.”
Galamukani! Oct. 8
“Masiku ano zikuoneka kuti mabanja a kholo limodzi lokha akuchuluka kwambiri. Baibulo limasonyeza kuti Mlengi wathu amawamvera chisoni mabanja otereŵa. [Ŵerengani Salmo 146:9.] Galamukani! iyi ikusonyeza momwe mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zingathandizire makolo ameneŵa kulera ana awo bwinobwino.”