Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct.15
“Popeza Mulungu ali kumwamba, ena amaganiza kuti n’zosatheka kum’dziwa bwino. Kodi munayamba mwaganizapo choncho? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yohane 17:3.] Magazini ino ikulongosola mmene tingam’dziwire bwino Mulungu.”
Galamukani! Oct.
“Ambirife taferedwapo anthu amene tinali kuwakonda. Kodi mukuganiza kuti pali zinthu zomwe tingachite kuti tithandize anthu akufawa? [Yembekezani ayankhe.] Magazini ino ili ndi yankho la m’Baibulo la funso limenelo. Ikulongosolanso lonjezo lotonthoza ili.” Werengani Yohane 5:28, 29. Ndiyeno pitani pa nkhani yomwe ikuyambira pa tsamba 10.
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Masiku ano, pali maganizo osiyanasiyana pankhani yolera ana. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kuti makolo apeze malangizo odalirika pa nkhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Salmo 32:8.] Magazini iyi ili ndi malangizo abwino a m’Baibulo pa nkhani yolera ana.”
Galamukani! Nov.
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti ngati Mulungu wachikondi, wachilungamo ndi wamphamvu alipodi, n’chifukwa chiyani pali mavuto ochuluka chonchi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zomwe lemba ili limanena za yemwe amayambitsa kuvutika. [Werengani 1 Yohane 5:19.] Magazini ino ikulongosola mfundo za m’Baibulo zosonyeza zomwe Mulungu akuchita kuti athetse mavuto.”