Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct. 15
“Zinthu zambiri zimene timasankha zimakhudza moyo wathu kwa nthaŵi yaitali. Kodi n’chiyani chingatithandize kupeŵa kusankha molakwika? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 3:6.] Magazini ya Nsanja ya Olonda iyi ili ndi mfundo zisanu zochokera m’Baibulo zimene zingatithandize kusankha mwanzeru.”
Galamukani! Oct. 8
“Timachita chidwi kwambiri tikaona mmene zinyama zimalankhulirana. Koma kodi mukudziŵa kuti m’njira zina anthu ndi apadera? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Salmo 65:2.] Mosiyana ndi zinyama, timalakalaka kulankhula ndi Mulungu. Magazini iyi ikufotokoza mmene tingamalankhulirane bwino ndi anthu komanso ndi Mulungu.”
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Tonsefe nthaŵi inayake munthu amene tinkamukhulupirira anatikhumudwitsapo. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi pali winawake amene ndingamukhulupirire?’ [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 3:5.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake tingakhulupirire Mulungu ndi mtima wathu wonse. Ikufotokozanso mmene tingadziŵire anthu amene tingawakhulupiriredi.”
Galamukani! Oct. 8
“Kodi mwamva zoti alimi ambiri zikuwavuta kuti azidalira ulimi pa moyo wawo? [Yembekezani ayankhe.] Magazini ya Galamukani! iyi ikufotokoza za vuto limeneli komanso za lonjezo limene lili m’Baibulo loti zinthu zisintha m’tsogolo muno. [Ŵerengani Salmo 72:16.] Ndikadzabweranso, ndikufuna ndidzakufotokozereni mmene Mulungu adzachitire zimenezi.”