Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct. 15
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti atakhala ndi ndalama zambiri m’pamenenso angakhale ndi moyo wabwino. Kodi inu mukuganiza kuti zimenezo n’zoona? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene analemba mwamuna wina amene anali wolemera kwadzaoneni. [Ŵerengani Mlaliki 5:10.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zimene zimaposa chuma.”
Galamukani! Nov 8
“Makolo ambiri amaona kuti n’kwabwino kuphunzitsa ana akadali aang’ono. Kodi mumaona zimenezi kukhala zofunika masiku ano? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 22:6.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza zinthu zenizeni zimene makolo angachite kuti athandize ana awo kukula bwino ndi kudzakhala achikulire odalirika.”
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Anthu ambiri sakhulupirira kuti atsogoleri ali ndi mphamvu yoti angathetse mavuto amene alipo masiku ano. Kodi mukuganiza kuti pali aliyense amene angachite zimene anazinena m’mavesi awazi? [Ŵerengani Salmo 72:7, 12, 16. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza za mtsogoleri ameneyu kuti ndani ndiponso zimene adzachita.”
Galamukani! Nov. 8
“Ana amafunika malangizo kuti athane ndi zovuta zimene amakumana nazo masiku ano, kodi si zoona zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Aefeso 6:4.] Magazini iyi ikufotokoza zimene chilangizo chimatanthauza. Ikulongosolanso mmene makolo angaperekere malangizo ndi mmene angawongolere ana awo popanda kuwakwiyitsa.”