Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/05 tsamba 8
  • Zimene Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 10/05 tsamba 8

Zimene Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda Oct. 15

“Anthu ambiri amaona maphunziro monga njira yopezera moyo wabwino. Kodi mukuganiza kuti alipo maphunziro amene angamuthandize munthu kukhala wabwino ndi kumuthandiza kupirira mavuto? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aroma 12:2.] Magazini iyi ikufotokoza za mmene tingapindulire ndi maphunziro apamwamba kwambiri amene alipo lerolino.”

Galamukani! Nov. 8

“Anthu ambiri amakonda kuwerenga nyuzipepala pafupifupi tsiku lililonse. Kodi mukuganiza kuti tiyenera kukhulupirira zimene nyuzipepala zimalemba? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ili ndi mfundo zoti zizikuthandizani kupindula mukamawerenga nyuzipepala. Ikufotokozanso chifukwa chake muyenera kukhala osamala pamene mukuwerenga nyuzipepala.” Werengani Miyambo 14:15.

Nsanja ya Olonda Nov. 1

“Anthu ambiri akuvutika chifukwa cha kusoweka kwa chilungamo padziko lapansi. Kodi mukuganiza kuti alipo wina aliyense amene angasinthe dziko kuti likhale labwino? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikunena za zinthu zimene zimalepheretsa kusinthaku. Ikufotokozanso za amene adzachotse zinthu zolepheretsa kusintha ndi zimene adzachite kuti padziko lapansi pakhale mtendere weniweni ndi chitetezo.” Werengani Salmo 72:12-14.

Galamukani! Nov. 8

“Padziko lonse lapansi pali kusiyana kwambiri pakati pa anthu olemera ndi anthu osauka. Kodi mukuganiza kuti tingatani kuti vuto limeneli lithe? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mateyu 6:9, 10.] Magazini iyi ikusonyeza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa vuto limene lilipo masiku ano la kusiyana pakati pa olemera ndi osauka.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena