Bokosi la Mafunso
◼ Kodi pali ubwino wanji wosonkhana ndi mpingo wa gawo limene tikukhala?
Kupyolera m’mipingo, timalimbikitsidwa ‘kufulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24, 25) Kupyolera mu mpingo timaphunzira choonadi ndipo timakhala okonzeka kukwaniritsa ntchito yathu yopanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Timalimbikitsidwanso kupirira ziyeso mokhulupirika ndipo tili ndi oyang’anira achikondi otithandiza kupambana polimbana ndi mavuto ndi nkhaŵa zimene zikuwonjezekawonjezekabe. N’zoonekeratu kuti mpingo ndi wofunika kuti tikhale olimba mwauzimu. Komabe, kodi kusonkhana ndi mpingo wa gawo limene tikukhala kuli ndi ubwino uliwonse?
Anthu angakhale ndi zifukwa zosiyanasiyana, monga ntchito, kukhala ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira ndiponso kayendedwe, zomwe zingakhudze zimene angasankhe pankhani ya mpingo umene azisonkhana. Komabe, pamene munthu asonkhana ndi mpingo wa gawo limene akukhala, amapindula kwambiri mwauzimu ndiponso mwanjira zina. Akulu angathe kulankhula ndi ofalitsa onse mofulumira zedi pakachitika zinthu zina zadzidzidzi. Bokosi la Mafunso la m’mbuyomo linanenanso ubwino wina wosonkhana ndi mpingo wa gawo limene tikukhala.—May 1991.
Nthaŵi zambiri, kumakhala kosavuta zedi kupita ku misonkhano yapafupi, zimatithandiza kufika nthaŵi yabwino moti titha kulankhula ndi anthu ena, kusamalira nkhani zina zofunika, ndi kuimba nawo nyimbo yotsegulira ndi pemphero. Ngati tapeza anthu achidwi m’dera lathulo, kaŵirikaŵiri sizitivuta kuwayendera, kuchita nawo phunziro la Baibulo ndiponso kuwasonyeza ku misonkhano imene sangavutike kufikapo.
Tili ndi chikhulupiriro kuti mitu ya mabanja ilingalira nkhaniyi mwapemphero, kuona bwinobwino mfundo zonse zofunika pamene ikusankha zinthu zothandiza moyo wauzimu ndi wakuthupi wa mabanja awo.—1 Tim. 5:8.