Kalata Yochokera ku Nthambi
Okondedwa ofalitsa Ufumu:
“Mulungu anakulitsa.” (1 Akor. 3:6) N’zosangalatsa kwambiri kuona kuwonjezeka kumene kwachitika m’gawo lino la dziko la Malawi. M’chaka chautumiki cha 2003, tinayambitsa maphunziro atsopano a Baibulo oposa 10,000. Tikuyamikira kwambiri zimenezi.
Popeza ku Malawi kuno tsopano kuli mipingo yopitirira 900, pakufunikabe Nyumba za Ufumu zina. Pamene timafika kumapeto kwa chaka chautumiki chapitachi Nyumba za Ufumu pafupifupi 650 zinali zitamangidwa. Tikukulimbikitsani abale ndi alongo, kuti mupitirizebe kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi kuthandiza anthu achidwi kuti azisonkhana nafe m’nyumba zokongola zolambiriramo zimenezi zimene zimaoneka bwino m’deralo.
Pofuna kusindikiza mabuku okwanira malinga ndi kuwonjezeka kwa padziko lonse, nyumba yosindikizira mabuku ya ku Watchtower Farms, yomwe ili pafupi ndi tauni ya Wallkill ku New York, ikuwonjezeredwa. Zinthu zikuyenda bwino pamene akuwonjezera nyumbayo yomwe itenge malo okwana mahekitala 1.4. Malo ameneŵa ndi ofanana ndi malo amene pangamangidwe Nyumba za Ufumu zazikulu ndithu zokwana 30! Makina aŵiri aakulu osindikizira amakono akuyembekezeka kufika kumayambiriro kwa chaka cha 2004. Makina alionse azidzasindikiza magazini okwana 25 pa sekondi. Mu 2004, adzaikanso makina atsopano omatira mabuku ndi othandiza pa ntchito yotumiza mabuku. Makina ameneŵa adzathandiza kupanga zinthu zambiri pamene anthu ogwira ntchito adzakhala ochepa.
Pamene tikuyamba chaka chautumiki cha 2004, tikupemphera nanu limodzi kuti Yehova apitirize ‘kukulitsa.’
Ndife abale anu,
Ofesi ya Nthambi ya Malawi.