“Kondani Yehova, Inu Nonse Okondedwa”
Chikumbutso cha Imfa ya Yesu Chidzachitika pa April 4
1 Zaka zam’mbuyomo, ku Ukraine panthaŵi yaulamuliro Wachikomyunizimu, akuluakulu aboma ankalondalonda kwambiri abale athu—makamaka tsiku la Mgonero wa Ambuye likayandikira—chifukwa ankafuna kupeza kumene akachitire mwambowu. Limeneli linali vuto la nthaŵi zonse, chifukwa akuluakulu a bomawo ankadziŵa tsiku la Chikumbutso likayandikira. Kodi abale akanatani? Nyumba ya mlongo wina inali ndi chipinda chapansi, chimene chinasefukira madzi kufika m’maondo. Popeza kuti akuluakulu a boma sankaganizira kuti anthu angasonkhane m’chipindacho, abale anamanga pulatifomu yaitali kupitirira munalekeza madziwo. Ngakhale kuti anakhala choŵerama papulatifomupo chifukwa chakuti denga linali pafupi, palibe anasokoneza pamene mpingowo unali kuchita mosangalala mwambo wa Chikumbutso.
2 Kulimba mtima kwa abale athu a ku Ukraine pomvera lamulo lokumbukira imfa ya Yesu, unali umboni wabwino kwambiri wakuti amakonda Mulungu. (Luka 22:19; 1 Yoh. 5:3) Tikakumana ndi zovuta pamoyo wathu, zitsanzo zimenezi zingatilimbikitse ndi kutithandiza kutsimikiza mtima kupezeka pamwambo wa Mgonero wa Ambuye pa April 4. Mwanjira imeneyi, timasonyeza kuti tili ndi maganizo a wamasalmo amene anaimba kuti: “Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake.”—Sal. 31:23.
3 Thandizani Ena Kukonda Kwambiri Mulungu: Kukonda Mulungu kumatipangitsanso kuitanira ena kudzachita nafe Chikumbutso. Mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2004 inalimbikitsa tonse kulemba mayina a anthu amene tikufuna kuwaitana ku Chikumbutso. Kodi mukuyesetsa kuuza munthu aliyense amene munam’lemba dzina? Pezani nthaŵi yowafotokozera chifukwa chake mwambowu uli wofunika kwa iwo. Kuwakumbutsa mokoma mtima zatsiku ndi nthaŵi ya Chikumbutso ndiponso, ngati n’kofunika, kudzipereka kudzayendera nawo limodzi kungawalimbikitse kudzapezekapo.
4 Pa Chikumbutso, tidzayesetse kuwapatsa moni amene tinawaitana, ndipo tidzawathandize kukhala omasuka. Kodi mungawathandize bwanji kukonda kwambiri Yehova? Khalani wokonzeka ndi wofunitsitsa kuyankha mafunso awo. Khalani wokonzeka kuwapempha kuphunzira nawo Baibulo ngati n’kotheka. Apempheni kupezeka pamisonkhano yathu yampingo yamlungu ndi mlungu. Makamaka akulu ayenera kusonyeza chidwi kwa Akristu osalalikira amene apezeka pa Chikumbutso. Angakonze zowayendera anthu ameneŵa ndi kuwalimbikitsa kuyambiranso kulalikira, akhoza kungowonjezera pa mfundo zimene zinakambidwa pankhani ya Chikumbutso.—Aroma 5:6-8.
5 Kukulitsa Kukonda Kwathu Yehova: Kulingalira mofatsa mphatso ya dipo kungakulitse kukonda kwathu Yehova ndi Mwana wake. (2 Akor. 5:14, 15) Munthu wina amene wakhala akupezeka pa Chikumbutso kwa zaka zambiri anati: “Timayembekezera mwachidwi nthaŵi ya Chikumbutso. Chaka chilichonse Chikumbutso chimakhala chapadera kwambiri kwa ife. Ndimakumbukira nditaima m’nyumba yamaliro zaka 20 zapitazo, ndikuyang’ana mtembo wa atate wanga okondedwa ndipo ndinayamba kuyamikira dipo ndi mtima wonse. Zisanachitike zimenezi dipo linali nkhani imene ndinali kungoidziŵa chabe. Ndinkadziŵa malemba onse okhudza dipo ndiponso mmene ndingafotokozere malembawo. Koma pamene ndinakhudzidwa kwambiri ndi imfa mpamene mtima wanga unasangalaladi ndi zimene zidzachitika chifukwa cha dipo lamtengo wapatali limenelo.”—Yoh. 5:28, 29.
6 Pamene tsiku la Chikumbutso cha chaka chino likuyandikira, khalani ndi nthaŵi ‘yokonzekeretsa mtima wanu.’ (2 Mbiri 19:3, NW) Sinkhasinkhani kuŵerenga Baibulo kwapadera kwa panthaŵi ya Chikumbutso, kopezeka m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2004 ndi pa Kalendala ya 2004. Ena amakonda kuŵerenga mutu 112 mpaka 116 mu buku la Munthu Wamkulu panthaŵi ya phunziro la banja. Anthu ena amafufuza mfundo zina pogwiritsa ntchito zida zina zophunzirira zoperekedwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Mat. 24:45-47) Tonse tingatchule mphatso ya dipo m’mapemphero athu apansi pamtima. (Sal. 50:14, 23) Inde, panyengo ino ya Chikumbutso, tipitirizetu kulingalira chikondi cha Yehova pa ife ndipo tifufuze njira zimene tingasonyezere kuti timamukonda.—Marko 12:30; 1 Yoh. 4:10.