Chakudya Chauzimu Chapanthaŵi Yake
1. Kodi Ezekieli 36:29 akukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
1 ‘Ndidzaitana tirigu ndi kum’chulukitsa, sindidzaikira inu njala,’ anatero Ambuye Mfumu Yehova. (Ezek. 36:29) Mawu aulosi ameneŵa akunena za anthu a Mulungu masiku ano. Mophiphiritsira, Yehova wameretsera anthu ake tirigu wambiri zedi wopatsa moyo. Chakudya chauzimu chapanthaŵi yake chimene chimaperekedwa kudzera m’misonkhano yathu yachigawo chikuchitira umboni kwambiri mfundo imeneyi.
2. Kodi Yehova wagwiritsa ntchito bwanji misonkhano yachigawo kupereka chakudya chauzimu chapanthaŵi yake?
2 Pamsonkhano umene unachitikira ku Columbus, Ohio, mu 1931, Yehova analangiza olambira ake kutenga dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Mu 1935 khamu lalikulu la pa Chivumbulutso 7:9-17 linadziŵika bwino. Mu 1942, Mbale Knorr anakamba nkhani yakuti “Mtendere—Kodi Ungakhalitse?” Nkhani imeneyi inalimbikitsa ntchito yolalikira ya padziko lonse ndipo inapangitsa kuti atsegule Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Ngakhale kuti misonkhano ina yachigawo imakhala yosaiŵalika kwambiri, uliwonse umakhala gome lodzala ndi chakudya chauzimu chopatsa thanzi choperekedwa panthaŵi yake.—Sal. 23:5; Mat. 24:45.
3. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipindule ndi phwando lauzimu pamsonkhano wathu wachigawo?
3 Kodi Mukudya Bwino? N’zotheka kukhala ndi chakudya chambiri koma n’kumasoŵa chakudya m’thupi ngati sitikudya chakudyacho. (Miy. 26:15) N’chimodzimodzinso mwauzimu. Pamisonkhano ingapo, tinaona anthu ambiri akuyendayenda popanda chifukwa chenicheni kapena akulankhulana pulogalamu ili m’kati. Ngakhale kuti kucheza nkhani zolimbikitsa ndi mbali yofunika pamsonkhano wachigawo, nthaŵi yake ndi chigawo chilichonse chisanayambe kapena chikatha. (Mlal. 3:1, 7) Ngati sitinakhale pansi n’kumamvetsera mwatcheru, tingaphonye mfundo yofunika kwambiri. Nthaŵi zina oyang’anira madipatimenti apamsonkhano wachigawo ndi abale amene ali ndi ntchito zina pamsonkhano angafunike kukambirana nkhani zokhudza msonkhanowo mapulogalamu ali m’kati. Ngati sakukambirana nkhani zokhudza msonkhano, ayenera kupereka chitsanzo chabwino mwa kumvera mwatcheru mapulogalamu. Aliyense wa ife sayenera kuphonya mbali ina ya chakudya chauzimu chimene chimaperekedwa.—1 Akor. 10:12; Afil. 2:12.
4. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira chakudya chauzimu chochuluka chimene Yehova akupereka?
4 Timasangalala kwambiri ndi mfundo zauzimu zochuluka zimene Yehova akupereka, poyerekeza ndi ziphunzitso za Matchalitchi Achikristu zomwe n’zosathandiza! (Yes. 65:13, 14) Njira imodzi imene tingasonyezere ‘kuyamikira’ ndiyo yoona msonkhano wachigawo kukhala mpata woti tiphunzitsidwe ndi Yehova. (Akol. 3:15) Maganizo athu azikhala pa zimene zikunenedwa osati pa wokambayo, ndipo onani uthengawo kuti ukuchokera kwa ‘mphunzitsi’ wathu Wamkulu. (Yes. 30:20, 21; 54:13) Mvetserani mwatcheru. Lembani mwachidule notsi za mfundo zazikulu. Madzulo aliwonse onaninso mfundo zazikulu za pulogalamu yatsikulo. Gwiritsani ntchito zimene mukuphunzira.
5. Kodi misonkhano yachigawo imatipatsa zifukwa zotani zokhalira osangalala?
5 Msonkhano wachigawo uliwonse wochitika Armagedo isanachitike, kaya ukuchitikira ku msasa wa anthu othaŵa kwawo, m’dziko limene muli nkhondo, kapena pamalo aakulu abata amene anthu asonkhana, kumakhala kugonjetsa Satana! Monga abale ogwirizana, timasangalala ndi mwayi umene tili nawo wosonkhana pamodzi pamisonkhano yachigawo. (Ezek. 36:38) Tili ndi chidaliro chakuti Yehova atipatsanso mwachikondi ‘phoso la panthaŵi yake.’—Luka 12:42.
[Bokosi patsamba 4]
Sonyezani Kuyamikira Gome la Yehova
◼ Mvetserani mwatcheru
◼ Lembani mfundo zazikulu
◼ Onaninso mfundo zazikulu za pulogalamu yatsikulo madzulo aliwonse
◼ Gwiritsani ntchito zimene mukuphunzira