Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 9
Kukonzekeretsa Ophunzira Kuti Adziwe Kulalikira Mwamwayi
1 Pamene Andreya ndi Filipo anazindikira kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa, anakanika kuti angokhala osauza ena za nkhani yosangalatsayi. (Yoh. 1:40-45) Chimodzimodzinso masiku ano, ophunzira Baibulo akayamba kukhulupirira zimene akuziphunzira, amafunitsitsa kuuza anthu ena zimene akuphunzirazo. (2 Akor. 4:13) Kodi tingawalimbikitse bwanji kuchita ulaliki wa mwamwayi ndiponso kuti aziuchita mogwira mtima?
2 Mukhoza kum’funsa wophunzirayo ngati walankhulapo kwa ena zimene waziphunzira m’Baibulo. Mwina pangakhale anzake kapena ena apabanjapo amene atha kuwaitana kuti adzakhale naye limodzi pamene akuphunzira. M’funseni ngati pali anthu ena monga anzake a kuntchito, kaya anzake a kusukulu, kapenanso anthu ena achinansi amene asonyezapo chidwi pa zimene akuphunzira. Mwanjira imeneyi mukhoza kum’thandiza kuyamba kulalikira. M’thandizeni kuzindikira chifukwa chake ayenera kukhala womvetsetsa ndiponso waulemu ndi wachifundo pamene akulankhula ndi ena za Yehova Mulungu ndi zolinga zake.—Akol. 4:6; 2 Tim. 2:24, 25.
3 Kuuza Ena Zimene Amakhulupirira: Kuphunzitsa ophunzira Baibulo kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pamene akuuza ena zimene amakhulupirira n’chinthu chofunika kwambiri. Pamene mukuphunzira, mukafika pa mfundo zina m’funseni wophunzirayo mafunso ngati akuti: “Kodi mungagwiritse ntchito bwanji Baibulo kuti mufotokoze mfundo yoona iyi kwa a m’banja mwanu?” kapena “Kodi ndi lemba liti la m’Baibulo limene mungagwiritse ntchito kum’tsimikizira mnzanu kuti mfundo iyi ndi yoona?” Muoneni mmene akuyankhira, ndipo m’sonyezeni zimene angachite kuti zimene akuphunzitsanzo zizichokera m’Malemba. (2 Tim. 2:15) Mwa kuchita zimenezi, mudzakhala mukum’konzekeretsa wophunzirayo ponse pawiri kulalikira mwamwayi ndiponso kuti akadzayenerera adzathe kugwira ntchito yolalikira ndi mpingo.
4 Ndi bwinonso kuthandiza ophunzira Baibulo athu kuti akhale okonzeka kukumana ndi chitsutso. (Mat. 10:36; Luka 8:13; 2 Tim. 3:12) Ngati ena afunsa funso kapena kunena ndemanga zina zokhudza Mboni za Yehova, umenewu ungakhale mpata woti ophunzira athe kulalikira. Bulosha lakuti Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? likhoza kuwathandiza kukhala “okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira.” (1 Pet. 3:15) Lili ndi mfundo zolondola zoti atsopano akhoza kuzigwiritsa ntchito kuthandizira anzawo ndiponso a m’banja mwawo amene akuwafunira zabwino, kuti athe kumvetsa zikhulupiriro ndi ntchito zathu zochokera m’Baibulo.