Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June 15
“Ambirife, mbali yaikulu ya moyo wathu idzathera kugwira ntchito. Ena amaona zimenezi monga dalitso, koma ena amaziona ngati ndi temberero. Kaya inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mlaliki 2:24.] Magazini iyi ikusonyeza mmene Baibulo lingatithandizire kuona ntchito m’njira yoyenera. Ikufotokozanso mmene tingachitire ndi mavuto ena akuntchito.”
Galamukani! July 8
“Kodi mukuganiza kuti dera lathu lino likanakhala malo abwino kukanakhala kuti aliyense akutsatira mawu awa? [Werengani Aefeso 4:28. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto amene aliyense wa ife amakumana nawo chifukwa cha anthu oba zinthu m’masitolo. Ikufotokozanso mmene kuba zinthu m’masitolo, pamodzi ndi makhalidwe ena oipa zidzakhalire mbiri yakale posachedwapa.”
Nsanja ya Olonda July 1
“Tonsefe timadziwa za anthu amene amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino komano amaoneka kuti akusowekabe chinachake pa moyo wawo. Kodi mukuganiza kuti amakhala akufuna chiyani? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mateyu 5:3.] Magazini iyi ikufotokoza njira yofunika kwambiri imene tingapezere mtendere wa m’maganizo. Njira yake ndiyo kukhutiritsa njala yathu yauzimu.”
Galamukani! July 8
“Masiku ano pamene anthu ali pa mpikisano wofunafuna ntchito, kusowa ntchito ndi vuto lalikulu kwambiri. Magazini iyi ili ndi njira zisanu zimene zingakuthandizeni kupeza ntchito. [Muwerengereni timitu ting’onoting’ono tomwe tili m’nkhani yakuti “Njira Zisanu za Mmene Mungapezere Ntchito.”] Ilinso ndi mfundo zothandiza pa zimene mungachite kuti musataye mwayi wanu wa ntchito.” Werengani Miyambo 22:29, limene mawu ake ali patsamba 10.